YouVersion Logo
Search Icon

OWERUZA 17

17
Mika ndi fano lake
1Ndipo ku mapiri a Efuremu kunali munthu dzina lake ndiye Mika. 2Ndipo iye anati kwa amai wake, Ndalama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m'makutu mwanga, taonani ndalamazo ndili nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wake anati, Yehova adalitse mwana wanga. 3#Eks. 20.4; Lev. 19.4Nabwezera amake ndalama zija mazana khumi ndi limodzi; nati amai wake, Kupatula ndapatulira Yehova ndalamazo zichoke ku dzanja langa, zimuke kwa mwana wanga, kupanga nazo fano losema ndi fano loyenga; m'mwemo ndikubwezera izi. 4Ndipo pamene anambwezera mai wake ndalamazo, mai wake anatapako ndalama mazana awiri, nazipereka kwa woyenga, ndiye anazipanga fano losema ndi fano loyenga; ndipo linakhala m'nyumba ya Mika. 5#1Maf. 13.33Koma munthuyu Mika anali nayo nyumba ya milungu, napanga chovala cha wansembe, ndi timafano, namninkha zansembe mwana wake wina wamwamuna, amene anakhala wansembe wake. 6#Deut. 12.8Masikuwa panalibe mfumu m'Israele, yense anachita chomuyenera m'maso mwake.
7Ndipo panali mnyamata wa ku Betelehemu-Yuda wa banja la Yuda, ndiye Mlevi, nagonera iye komweko. 8Adachokera munthuyo m'mudzi m'Betelehemu-Yuda, kugonera paliponse akapeza pokhala; ndi pa ulendo wake anafika ku mapiri a Efuremu, kunyumba ya Mika. 9Ndipo Mika ananena naye, Ufumira kuti? Nati kwa iye, Ndine Mlevi wa ku Betelehemu-Yuda, ndilikumuka kugonera kumene ndikapeza pokhala. 10#Gen. 45.8; Ower. 18.19Nanena naye Mika, Khalitsa nane, nukhale atate wanga, ndi wansembe wanga, ndipo ndidzakupatsa ndalama khumi pachaka, ndi chovala chofikira, ndi zakudya zako. Nalowa Mleviyo. 11Ndi Mleviyo anavomera kukhalitsa ndi munthuyo; ndi mnyamatayo anamkhalira ngati mmodzi wa ana ake. 12Ndipo Mika anamninkha zansembe Mleviyo, ndi mnyamatayo anakhala wansembe wake, nakhala m'nyumba ya Mika. 13Nati Mika, Tsopano ndidziwa kuti Yehova adzandichitira chokoma, popeza ndili naye Mlevi akhale wansembe wanga.

Currently Selected:

OWERUZA 17: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for OWERUZA 17