YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 64

64
1 # Mas. 144.5 Mwenzi mutang'amba kumwamba ndi kutsikira pansi, kuti mapiri agwedezeke pamaso panu; 2monga pamene moto uyatsa zitsamba, ndi moto uwiritsa madzi; kudziwitsa kwa amaliwongo anu dzina lanu, kuti amitundu anthunthumire pamaso panu. 3#Ower. 5.4-5Pamene Inu munachita zinthu zoopsa, zimene ife sitinayang'anira, Inu munatsika, mapiri anagwedezeka pamaso panu. 4#1Ako. 2.9Pakuti kuyambira kale anthu sanamve pena kumvetsa ndi khutu, ngakhale diso silinaone Mulungu wina popanda Inu, amene amgwirira ntchito iye amene amlindirira Iye. 5#Mac. 10.35Inu mukomana ndi iye amene akondwerera, nachita chilungamo, iwo amene akumbukira Inu m'njira zanu; taonani Inu munakwiya, ndipo ife tinachimwa; takhala momwemo nthawi yambiri, kodi tidzapulumutsidwa? 6#Mas. 90.5-6; Afi. 3.9Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse zili ngati chovala chodetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo. 7#Hos. 7.7Ndipo palibe amene aitana dzina lanu, amene adzikakamiza yekha kugwiritsa Inu; pakuti Inu mwatibisira nkhope yanu, ndipo mwatinyeketsa ndi zoipa zathu. 8#Yes. 63.16; Yer. 18.6; Aro. 9.20; Aef. 2.10Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu. 9#Mas. 74.1-2Musakwiye kopambana, Yehova, musakumbukire zoipa nthawi zonse; taonani, yang'anani ife, tikupembedzani Inu, ife tonse tili anthu anu. 10Midzi yanu yopatulika yasanduka chipululu, Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu wasanduka bwinja. 11#2Maf. 25.9Nyumba yathu yopatulika ndi yokongola, m'mene makolo athu anakutamandani Inu, yatenthedwa ndi moto; ndi zinthu zathu zonse zokondweretsa zapasuka. 12#Mas. 83.1Kodi mudzadziletsa pa zinthuzi, Yehova? Kodi Inu mudzakhala chete ndi kutivutitsa ife zolimba?

Currently Selected:

YESAYA 64: BLPB2014

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in