YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 61

61
Alalikira Uthenga Wabwino wa chipulumutso
1 # Luk. 4.18-19 Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende; 2ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro; 3#Mas. 30.11; Yes. 60.21ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe. 4#Yes. 58.12Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso midzi yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri. 5Ndipo alendo adzaimirira ndi kudyetsa magulu ako, ndi anthu akunja adzakhala olima ako, ndi kukukonzera minda yamphesa. 6#Yes. 60.5, 11-16; 1Pet. 2.9Koma inu mudzatchedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya chuma cha amitundu, nimudzalowa mu ulemerero wao. 7#Yes. 40.2; Zek. 9.12M'malo mwa manyazi anu, owirikiza; ndi chitonzo iwo adzakondwera ndi gawo lao; chifukwa chake iwo adzakhala nacho m'dziko mwao cholowa chowirikiza, adzakhala nacho chikondwerero chosatha. 8#Yes. 1.11, 13; 55.3Pakuti Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m'zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha. 9#Yes. 65.23Ndipo ana ao adzadziwidwa mwa amitundu, ndi obadwa ao mwa anthu; onse amene awaona adzawazindikira kuti iwo ndiwo ana amene Yehova wadalitsa.
10 # Mas. 132.9, 16; Hab. 3.18; Chiv. 21.2 Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Ine wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo. 11#Mas. 85.11; Yes. 62.7Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.

Currently Selected:

YESAYA 61: BLPB2014

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in