YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 56

56
Malonjezo a kwa iwo osunga Sabata
1 # Yes. 46.13; Mat. 3.2; Aro. 13.11-12 Atero Yehova, Sungani inu chiweruziro, ndi kuchita chilungamo; pakuti chipulumutso changa chili pafupi kudza, ndi chilungamo changa chili pafupi kuti chivumbulutsidwe. 2#Yes. 58.13Wodala munthu amene achita ichi, ndi mwana wa munthu amene agwira zolimba ichi, amene asunga Sabata osaliipitsa, nasunga dzanja lake osachita nalo choipa chilichonse. 3#Mac. 10.1-2, 34Mlendo amene wadziphatika yekha kwa Yehova asanene, kuti, Yehova adzandilekanitsa ndithu ndi anthu ake; pena mfule asanene, Taonani ine ndili mtengo wouma. 4#Yes. 58.13Pakuti atero Yehova kwa mifule imene isunga masabata, nisankha zinthu zimene zindikondweretsa Ine, nigwira zolimba chipangano changa, 5#Yoh. 1.12Kwa iyo ndidzapatsa m'nyumba yanga ndi m'kati mwa makoma anga malo, ndi dzina loposa la ana aamuna ndi aakazi; ndidzawapatsa dzina lachikhalire limene silidzadulidwa. 6#Yes. 58.13Alendonso amene adziphatika okha kwa Yehova, kuti amtumikire Iye, ndi kukonda dzina la Yehova, akhale atumiki ake, yense amene asunga sabata osaliipitsa, nagwira zolimba chipangano changa; 7#Mala. 1.11; Mat. 21.13; Aro. 12.1; 1Pet. 1.2naonso ndidzanka nao kuphiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m'nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zao zopsereza ndi nsembe zao zidzalandiridwa pa guwa la nsembe langa; pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse. 8#Mas. 147.2; Yoh. 10.16Ambuye Yehova amene asonkhanitsa otayika a Israele ati, Komabe ndidzasonkhanitsa ena kwa iye, pamodzi ndi osonkhanitsidwa akeake.
9Inu zilombo zonse za m'thengo, idzani kulusa, inde zilombo inu nonse za m'nkhalango. 10#Mat. 15.14; Afi. 3.2Alonda ake ali akhungu, iwo onse ali opanda nzeru; iwo onse ali agalu achete, osatha kuuwa; kungolota, kugona pansi, kukonda kugona tulo. 11#Yer. 23.1; Ezk. 34.2Inde agalu ali osusuka, sakhuta konse; amenewa ali abusa osazindikira; iwo onse atembenukira kunjira zao, yense kutsata phindu lake m'dera lake. 12#Yes. 28.7Idzani inu, ati iwo, ndidzatengera vinyo, ndipo tidzakhuta chakumwa chaukali; ndipo mawa kudzakhala monga tsiku lalero, tsiku lalikulu loposa ndithu.

Currently Selected:

YESAYA 56: BLPB2014

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in