YESAYA 52:14-15
YESAYA 52:14-15 BLPB2014
Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israele, momwemo nkhope yake yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu aliyense, ndi maonekedwe ake kupambana ana a anthu; momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwa kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira.





