YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 43

43
Mulungu Yehova yekha apulumutsa Israele
1 # Yes. 44.6 Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israele, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga. 2#Mas. 66.12; Dan. 3.25, 27Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha. 3Chifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israele, Mpulumutsi wako; ndapatsa Ejipito dombolo lako, Etiopiya ndi Seba m'malo mwako. 4Pokhala iwe wa mtengo wapatali pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako. 5#Yes. 41.10Usaope; pakuti Ine ndili ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kuchokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kuchokera kumadzulo. 6Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kumwera, Usaletse; bwera nao ana anga amuna kuchokera kutali, ndi ana anga akazi kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; 7#Yak. 2.7; 2Ako. 5.17-18; Aef. 2.10yense wotchedwa dzina langa, amene ndinamlenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye. 8Tulutsani anthu akhungu, amene ali ndi maso, ndi agonthi, amene ali ndi makutu. 9#Yes. 41.21-22, 26Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo anganene ichi ndi kuonetsa ife zinthu zakale? Atenge mboni zao, kuti avomerezeke ndi olungama; pena amve, nanene zoonadi. 10#Yes. 41.4; 42.1; Yoh. 15.27Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina. 11#Hos. 13.4Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha. 12#Yes. 43.10Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu. 13#Yoh. 8.58Inde chiyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m'dzanja langa; ndidzagwira ntchito, ndipo ndani adzaletsa?
14Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israele: Chifukwa cha inu ndatumiza ku Babiloni, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Ababiloni m'ngalawa za kukondwa kwao. 15Ine ndine Yehova Woyera wanu, Mlengi wa Israele, Mfumu yanu. 16#Eks. 14.16, 22; Yos. 3.13, 16Atero Yehova, amene akonza njira panyanja, ndi popita m'madzi amphamvu; 17amene atulutsa galeta ndi kavalo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi. 18Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale. 19#Eks. 17.6; Num. 20.11; 2Ako. 5.17; Chiv. 21.5Taonani, Ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m'chipululu, ndi mitsinje m'zidalala. 20Nyama za m'thengo zidzandilimekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; chifukwa ndipatsa madzi m'chipululu, ndi mitsinje m'mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika; 21#Aef. 1.5-6anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga. 22#Mik. 6.3; Mala. 1.13Komabe iwe sunandiitane Ine, Yakobo; koma iwe walema ndi Ine, Israele. 23#Amo. 5.25Iwe sunanditengere Ine zoweta zazing'ono za nsembe zopsereza zako; kapena kundilemekeza ndi nsembe zako. Sindinakutumikiritsa ndi nsembe zaufa, kapena kukutopetsa ndi lubani. 24#Mala. 2.17Iwe sunandigulire Ine nzimbe ndi ndalama, pena kundikhutitsa ndi mafuta a nsembe zako. Koma iwe wanditumikiritsa ndi machimo ako, wanditopetsa ndi mphulupulu zako. 25#Yer. 31.34; 50.20; Ezk. 36.22-23; Mac. 3.19Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako. 26#Yes. 1.18Undikumbutse Ine; tiyeni, tinenane pamodzi; fotokoza mlandu wako, kuti ukalungamitsidwe. 27Atate wako woyamba anachimwa, ndi otanthauzira ako andilakwira Ine. 28#Yer. 24.9Chifukwa chake ndidzaipitsa akulu a Kachisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israele akhale chitonzo.

Currently Selected:

YESAYA 43: BLPB2014

Highlight

Copy

Compare

Share

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in