YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 24

24
Chilango cha Mulungu cha pa dziko la Israele, ndi pa dziko lonse lapansi
1Taonani, Yehova apululutsa dziko, nalipasula, nalitembenuza dodolido, nabalalitsa okhalamo ake. 2#Ezk. 7.12-13; Hos. 4.9Ndipo padzakhala monga ndi anthu, moteronso ndi ansembe; monga ndi mtumiki, moteronso ndi mbuyake; monga ndi mdzakazi, moteronso ndi mbuyake wamkazi; monga ndi wogula, moteronso ndi wogulitsa; monga ndi wobwereka, moteronso ndi wombwereka; monga ndi wotenga phindu, moteronso ndi wombwezera phindu kwa iye. 3Dziko lidzapululuka konse, ndi kupasulidwa ndithu; pakuti Yehova anenana mau amenewa. 4Dziko lirira nilifota, dziko lilefuka nilifota, anthu omveka a padziko alefuka. 5#Gen. 3.17Dzikonso laipitsidwa ndi okhalamo ake omwe, chifukwa iwo alakwa pamalamulo nasinthanitsa malemba, nathyola chipangano cha nthawi zonse. 6#Mala. 4.6Chifukwa chake chitemberero chadya dziko, ndi amene akhala m'menemo apezedwa ochimwa, chifukwa chake okhalamo a padziko atenthedwa, ndipo anthu owerengeka atsala. 7Vinyo watsopano alira, mpesa ulefuka, mitima yonse yokondwa iusa moyo. 8#Yer. 7.34; Chiv. 18.22Kusangalala kwa mangaka kwalekeka, phokoso la iwo amene asekera litha, kukondwa kwa mngoli kwalekeka. 9Iwo sadzamwa vinyo ndi kuimba nyimbo; chakumwa chaukali chidzawawa kwa iwo amene achimwa. 10Mudzi wosokonezeka wagwetsedwa pansi; nyumba zonse zatsekedwa, kuti asalowemo munthu. 11Muli mfuu m'makwalala chifukwa cha vinyo; kukondwa konse kwadetsedwa, kusangalala kwa dziko kwatha. 12M'mudzi mwatsala bwinja, ndi chipata chamenyedwa ndi chipasuko. 13#Yes. 17.5-6Chifukwa chake padzakhala chotero pakati pa dziko mwa anthu, ngati kugwedeza kwa mtengo wa azitona, ngati khunkha la mphesa, pakutha masika ake. 14Amenewa adzakweza mau ao, nadzafuula; chifukwa cha chifumu cha Yehova, iwo adzafuula zolimba panyanja. 15Chifukwa chake lemekezani inu Yehova kum'mawa, ngakhale dzina la Yehova, Mulungu wa Israele, m'zisumbu za m'nyanja.
16 # Yer. 5.11 Kuchokera ku malekezero a dziko ife tamva nyimbo zolemekeza wolungama. Koma ine ndinati, Ndaonda ine, ndaonda ine, tsoka kwa Ine! Amalonda onyenga amangonyenga; inde ogulitsa onyenga apambana kunyenga. 17#Amo. 5.19Mantha ndi dzenje ndi msampha zili pa iwe, wokhala m'dziko. 18Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsa, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka. 19#Yer. 4.23Dziko lapansi lasweka ndithu, dziko lapansi lasungunukadi, dziko lapansi lili kugwedezeka kopambana. 20Dziko lapansi lidzachita dzandidzandi, ngati munthu woledzera, ndi kunjenjemera, ngati chilindo; ndi kulakwa kwake kudzalilemera, ndipo lidzagwa losaukanso.
21Ndipo padzali tsiku limenelo, kuti Yehova adzazonda kumwamba khamu lakumwamba, ndi mafumu a dziko lapansi. 22Ndipo iwo adzasonkhanitsidwa pamodzi, monga ndende zimasonkhanitsidwa m'dzenje, ndi kutsekeredwa m'kaidi, ndipo atapita masiku ambiri adzawazonda. 23#Yow. 2.31; Chiv. 19.4-6Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira chaulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi m'Yerusalemu, ndi pamaso pa akuluakulu ake.

Currently Selected:

YESAYA 24: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in