YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 15

15
Aneneratu za kuonongeka kwa Mowabu
1 # Yer. 48 Katundu wa Mowabu. Pakuti usiku umodzi Ari wa ku Mowabu wapasuka, nakhala chabe; usiku umodzi Kiri wa Mowabu wapasuka, nakhala chabe. 2#Deut. 34.1; Ezk. 7.18Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa. 3M'makwalala mwao adzimangira chiguduli m'chuuno, pamwamba pa nyumba zao, ndi m'malo a mabwalo ao, yense akuwa, naliritsa kwambiri. 4Ndi Hesiboni afuula zolimba, ndi Eleyale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; chifukwa chake amuna ankhondo a Mowabu afuula zolimba; moyo wake wanthunthumira m'kati mwake. 5Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko. 6Pakuti pa madzi a Nimurimu padzakhala mabwinja; popeza udzu wafota, msipu watha. 7Chifukwa chake zochuluka adazipeza, ndi zosungidwa zao adzazitenga kunka nazo kumtsinje wa mabango. 8Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Mowabu; kukuwa kwake kwafikira ku Egilaimu, ndi kukuwa kwake kwafikira ku Beerelimu. 9#2Maf. 17.25Pakuti madzi a Diboni adzala mwazi; pakuti ndidzatengera zina pa Diboni, mkango pa iye amene anapulumuka ku Mowabu, ndi pa otsala a m'dziko.

Currently Selected:

YESAYA 15: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in