YouVersion Logo
Search Icon

HOSEYA 12

12
Mlandu wa Yehova pa Israele ndi Yuda
1 # Hos. 11.12 Efuremu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse achulukitsa mabodza ndi chipasuko, ndipo achita pangano ndi Asiriya, natenga mafuta kunka nao ku Ejipito. 2#Mik. 6.2Ndipo Yehova ali ndi mlandu ndi Yuda, nadzalanga Yakobo monga mwa njira zake, adzambwezera monga mwa machitidwe ake. 3#Gen. 25.26; 32.28M'mimba anagwira kuchitende cha mkulu wake, ndipo atakula mphamvu analimbana ndi Mulungu; 4#Gen. 28.12, 19; 32.28inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Betele, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife; 5ndiye Yehova Mulungu wa makamu, chikumbukiro chake ndi Yehova. 6#Mik. 6.8M'mwemo utembenukire kwa Mulungu wako, sunga chifundo ndi chiweruzo, nuyembekezere Mulungu wako kosalekeza.
7 # Miy. 11.1 Ndiye Mkanani, m'dzanja lake muli miyeso yonyenga, akonda kusautsa. 8#Chiv. 3.17Ndipo Efuremu anati, Zedi ndasanduka wolemera, ndadzionera chuma m'ntchito zonse ndinazigwira; sadzapeza mwa ine mphulupulu yokhala tchimo. 9Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako chichokere dziko la Ejipito, ndidzakukhalitsanso m'mahema, monga masiku a zikondwerero zoikika. 10#2Maf. 17.13Ndalankhulanso ndi aneneri, ndipo Ine ndachulukitsa masomphenya; ndi pa dzanja la aneneri ndinanena ndi mafanizo. 11Kodi Giliyadi ndiye wopanda pake? Akhala achabe konse; m'Giligala aphera nsembe ya ng'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'michera ya munda. 12#Gen. 28.5; 29.20, 28Ndipo Yakobo anathawira kuthengo la Aramu, ndi Israele anagwira ntchito chifukwa cha mkazi, ndi chifukwa cha mkazi anaweta nkhosa. 13#Eks. 12.50-51Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israele kuchokera m'Ejipito, ndi mwa mneneri anasungika. 14#2Maf. 17.11-18Efuremu wautsa mkwiyo wowawa, m'mwemo Iye adzamsiyira mwazi wake, ndi Ambuye wake adzambwezera chomtonza chake.

Currently Selected:

HOSEYA 12: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in