HOSEYA 11
11
Kusayamika kwa Israele; machenjezo ndi malonjezo
1 #
Eks. 4.22-23
Pamene Israele anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali m'Ejipito. 2#2Maf. 17.16Monga anawaitana, momwemo anawachokera; anaphera nsembe Abaala, nafukizira mafano osema. 3Koma Ine ndinaphunzitsa Efuremu kuyenda, ndinawafungata m'manja mwanga; koma sanadziwe kuti ndinawachiritsa. 4#Mas. 78.24, 29; Yer. 31.3Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za chikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira chakudya. 5Iye sadzabwerera kunka kudziko la Ejipito, koma Asiriya adzakhala mfumu yake, popeza anakana kubwera. 6Ndi lupanga lidzagwera midzi yake, lidzatha mipiringidzo yake, ndi kuononga chifukwa cha uphungu wao. 7#Yer. 3.6Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m'mbuyo kundileka Ine; chinkana akawaitana atsate Iye ali m'mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense. 8#Mat. 23.37Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi. 9#Yes. 55.8-9Sindidzachita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efuremu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mudzi. 10#Yes. 31.4Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kuchokera kumadzulo. 11Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Ejipito, ndi ngati nkhunda m'dziko la Asiriya; ndipo ndidzawakhalitsa m'nyumba zao, ati Yehova 12Efuremu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israele ndi chinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.
Currently Selected:
HOSEYA 11: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: