YouVersion Logo
Search Icon

AGALATIYA Mau Oyamba

Mau Oyamba
Pamene uthenga wabwino wonena za Yesu unayamba kulalikidwa ndi kulandiridwa pakati pa anthu amene sanali Ayuda, funso lalikulu limene limafunsidwa linali lakuti kodi ndikoyenera kuti munthu atsatire Malamulo a Mose ngati akufuna mkhristu? Paulo ananena kuti izi sizinali zoyenera. Iye anatinso chofunika pa moyo wotsatira Khristu ndi ndicho chakuti anthu amalungamitsidwa ndi Mulungu pokhulupirira Khristu basi. Komabe pakati pa mipingo ya ku Galatiya, limene linali dera la ku Asiya, panali anthu amene anabwera ndi kumasutsana ndi Paulo ponena kuti munthu ayenera kutsata Malamulo a Mose ngati akufuna alungamitsidwe ndi Mulungu.
Kalata ya Paulo Mtumwi yolembera kwa Agalatiya inalembedwa pofuna kukonza chiphunzitso cholakwikachi chimene ena anabweretsa ndi kupotoza nacho anthu anzao. Paulo anayamba pa kuteteza udindo wake monga mtumwi wa Yesu Khristu. Iye anatsindika mfundo yakuti maitanidwe ake kukhala mtumwi anachokera kwa Mulungu, osati kwa munthu, ndiponso kuti utumiki wake unali wa kwa anthu sanali Ayuda. Kenaka akufotokoza kuti anthu amalungamitsidwa ndi Mulungu pokhapokha pamene akhulupirira. Mu mitu yomalizira, Paulo akutionetsa kuti khalidwe labwino la Chikhristu limachokera ku chikondi chimene chimapezeka pamene munthu wakhulupirira Yesu.
Za mkatimu
Mau oyamba 1.1-10
Ulamuliro wa Paulo pokhala mtumwi 1.11—2.21
Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu 3.1—4.31
Ufulu ndi udindo wa mkhristu 5.1—6.10
Mau omaliza 6.11-18

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in