YouVersion Logo
Search Icon

EKSODO 13

13
Ana oyamba kubadwa apatulidwira Yehova
1Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti, 2#Num. 3.13; Luk. 2.23Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.
3 # Eks. 23.15 Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka m'Ejipito, m'nyumba ya akapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa. 4Mutuluka lero lino mwezi wa Abibu. 5Ndipo kudzakhala atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, ndi la Ahiti, ndi la Aamori ndi la Ahivi, ndi la Ayebusi, limene analumbira ndi makolo ako kukupatsa, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, uzikasunga kutumikira kumeneku mwezi uno. 6Masiku asanu ndi awiri uzikadya mkate wopanda chotupitsa, ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri likhale la madyerero a Yehova; 7Azikadya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiriwo ndipo kasaoneke kanthu ka chotupitsa kwanu; inde chotupitsa chisaoneke kwanu m'malire ako onse. 8Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero chifukwa chomwe Yehova anandichitira ine potuluka ine m'Ejipito. 9#Yes. 49.16Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro pa dzanja lako, ndi chikumbutso pakati pa maso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa m'Ejipito ndi dzanja lamphamvu. 10Chifukwa chake uzikasunga lemba ili pa nyengo yake chaka ndi chaka.
11Ndipo kudzakhala, atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, monga anakulumbirira iwe ndi makolo ako, ndipo anakupatsa ilo, 12kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nao odzera kwa zoweta; amunawo ndi a Yehova. 13#Num. 18.15Koma woyamba yense wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ndipo ukapanda kumuombola uzimthyola khosi; koma oyamba onse a munthu mwa ana ako uziwaombola. 14Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa m'Ejipito, m'nyumba ya akapolo, ndi dzanja lamphamvu; 15ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; chifukwa chake ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola. 16#Eks. 13.9Ndipo chizikhala ngati chizindikiro pa dzanja lako, ndi chapamphumi pakati pa maso ako; pakuti Yehova anatitulutsa m'Ejipito ndi dzanja lamphamvu.
Ulendo wonka ku Nyanja Yofiira
17Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito. 18Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kuchipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israele anakwera kuchokera m'dziko la Ejipito okonzeka. 19#Gen. 50.25Ndipo Mose anamuka nao mafupa a Yosefe; pakuti adawalumbiritsatu ana a Israele ndi kuti, Mulungu adzakuzondani ndithu ndipo mukakwere nao mafupa anga osawasiya kuno. 20Ndipo anachokera ku Sukoti, nagona ku Etamu, pa malekezero a chipululu. 21#Eks. 40.38; Mas. 78.14; 105.39; Yes. 4.5Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m'njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku; 22sanachotse mtambo usana, kapena mtambo wamoto usiku, pamaso pa anthu.

Currently Selected:

EKSODO 13: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy