ESTERE 10
10
Ukulu wa Mordekai
1Ndipo mfumu Ahasuwero inasonkhetsa dziko, ndi zisumbu za ku nyanja. 2#Est. 9.4Ndi zochita zonse za mphamvu yake, ndi nyonga zake, ndi mafotokozedwe a ukulu wa Mordekai, umene mfumu inamkulitsa nao, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Mediya ndi Persiya? 3#Gen. 41.40; Neh. 2.10; Mas. 122.8-9Pakuti Mordekai Myuda anatsatana naye mfumu Ahasuwero, nakhala wamkulu mwa Ayuda, navomerezeka mwa unyinji wa abale ake wakufunira a mtundu wake zokoma, ndi wakunena za mtendere kwa mbeu yake yonse.
Currently Selected:
ESTERE 10: BLPB2014
Highlight
Share
Compare
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi