YouVersion Logo
Search Icon

DANIELE 7

7
Masomphenya a Daniele a zamoyo zinai ndi Nkhalamba ya kale lomwe
1Chaka choyamba cha Belisazara mfumu ya ku Babiloni Daniele anaona loto, naona masomphenya a m'mtima mwake pakama pake; ndipo analemba lotolo, nalifotokozera, mwachidule. 2Daniele ananena, nati, Ndinaona m'masomphenya anga usiku, taonani, mphepo zinai za mumlengalenga zinabuka pa nyanja yaikulu. 3#Chiv. 13.1Ndipo zinatuluka m'nyanja zilombo zazikulu zinai zosiyanasiyana. 4Choyamba chinanga mkango, chinali nao mapiko a chiombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zake zinathothoka, nichinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, nichinapatsidwa mtima wa munthu. 5Ndipo taonani, chilombo china chachiwiri chikunga chimbalangondo chinatundumuka mbali imodzi; ndi m'kamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake; ndipo anatero nacho, Nyamuka, lusira nyama zambiri. 6Pambuyo pake ndinapenya ndi kuona china ngati nyalugwe, chinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pake, chilombocho chinali nayonso mitu inai, nichinapatsidwa ulamuliro. 7Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano akulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi. 8Ndinali kulingilirira za nyangazi, taonani, pakati pa izo panaphuka nyanga ina, ndiyo yaing'ono; patsogolo pake zitatu za nyanga zoyambazi zinazulidwa ndi mizu yomwe; ndipo taonani, m'nyanga m'menemo munali maso ngati maso a munthu, ndi pakamwa palikunena zazikulu. 9Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pa mutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka. 10#Chiv. 20.4, 12Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa. 11Pamenepo ndinapenyera chifukwa cha phokoso la mau akulu idanena nyangayi; ndinapenyera mpaka adachipha chilombochi, ndi kuononga mtembo wake, ndi kuupereka utenthedwe ndi moto. 12Ndipo zilombo zotsalazo anazichotsera ulamuliro wao, koma anatalikitsa moyo wao, ukhalenso nyengo ndi nthawi. 13#Ezk. 1.26; Mat. 24.30Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake. 14#Mas. 2.6-8; 145.13; Mat. 11.27; Yoh. 3.35; 1Ako. 15.27-28Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.
Kumasulira kwa masomphenyawo
15Koma ine Daniele, mzimu wanga unalaswa m'kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m'mtima mwanga anandivuta. 16Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za choonadi za ichi chonse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwake kwa zinthuzi: 17#Dan. 7.3Zilombo zazikulu izi zinai ndizo mafumu anai amene adzauka pa dziko lapansi. 18#Yes. 60.12-14; 2Tim. 2.11-12Koma opatulika a Wam'mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, kunthawi zonka muyaya. 19Pamenepo ndinafuna kudziwa choonadi cha chilombo chachinai chija chidasiyana nazo zonsezi, choopsa chopambana, mano ake achitsulo, ndi makadabo ake amkuwa, chimene chidalusa, ndi kuphwanya, ndi kupondereza zotsala ndi mapazi ake; 20ndi za nyanga khumi zinali pamutu pake, ndi nyanga ina idaphukayi, imene zidagwa zitatu patsogolo pake; nyangayo idali ndi maso ndi pakamwa pakunena zazikulu, imene maonekedwe ake anaposa zinzake. 21#Chiv. 11.7Ndinapenya, ndipo nyanga yomweyi inachita nkhondo ndi opatulikawo, niwalaka, mpaka inadza Nkhalamba ya kale lomwe; 22#1Ako. 6.2; Chiv. 5.10ndi mlandu unakomera opatulika a Wam'mwambamwamba, nifika nthawi yakuti ufumu unali wao wa opatulikawo. 23Anatero, chilombo chachinai ndicho ufumu wachinai pa dziko lapansi, umene udzasiyana nao maufumu onse, nudzalusira dziko lonse lapansi, nudzalipondereza ndi kuliphwanya. 24Kunena za nyanga khumi, m'ufumu uwu adzauka mafumu khumi, ndi pambuyo pao idzauka ina; iyo idzasiyana ndi oyamba aja, nidzachepetsa mafumu atatu. 25#Chiv. 17.6Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam'mwambamwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam'mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi chilamulo; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lake mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu. 26#Dan. 7.10-22Koma woweruza mlandu adzakhalako, ndipo adzachotsa ulamuliro wake, kuutha ndi kuuononga kufikira chimaliziro. 27#Dan. 7.14, 18, 22; Luk. 1.33Ndipo ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse, zidzapatsidwa kwa anthu a opatulika a Wam'mwambamwamba; ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi maiko onse adzamtumikira ndi kummvera. 28Kutha kwake kwa chinthuchi nkuno. Ine Daniele, maganizo anga anandivuta kwambiri, ndi nkhope yanga inasandulika; koma ndinasunga chinthuchi m'mtima mwanga.

Currently Selected:

DANIELE 7: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy