YouVersion Logo
Search Icon

AMOSI 9

9
Masomphenya a kulangidwa koopsa
1Ndinaona Ambuye alikuima pa guwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwa iwo sadzapulumukadi. 2#Mas. 139.8-10Angakhale akumba mpaka kunsi kwa manda, dzanja langa lidzawatenga kumeneko; angakhale akwera kumwamba, ndidzawatsitsa komweko. 3Angakhale abisala pamwamba pa Karimele, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma. 4#Yer. 44.11Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwachitira choipa, si chokoma ai. 5Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzachita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m'nyanja; nilidzatsikanso ngati nyanja ya m'Ejipito; 6ndiye amene amanga zipinda zake zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lake pa dziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lake ndiye Yehova. 7#Eks. 20.2; Yer. 47.4Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israele? Ati Yehova. Sindinakweza Israele ndine, kumtulutsa m'dziko la Ejipito, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri? 8#Yer. 30.11Taonani, maso a Ambuye Yehova ali pa ufumu wochimwawo, ndipo ndidzauononga kuuchotsa pa dziko lapansi; pokhapo sindidzaononga nyumba ya Yakobo kuitha konse, ati Yehova. 9Pakuti taonani, ndidzalamulira, ndipo ndidzapeta nyumba ya Israele mwa amitundu onse, monga apeta tirigu m'lichero; koma silidzagwa pansi diso, ndi limodzi lonse. 10Ochimwa onse a anthu anga adzafa ndi lupanga, ndiwo amene akuti, Choipa sichidzatipeza, kapena kutidulira.
Lonjezo kuti madalitso adzabwera
11 # Mac. 15.16-17 Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zake; ndipo ndidzautsa zogumuka zake, ndi kuumanga monga masiku a kalelo; 12#Num. 24.18; Oba. 19kuti alandire otsala a Edomu akhale cholowa chao, ndi amitundu onse a kutchedwa dzina langa, ati Yehova wakuchita izi. 13#Lev. 26.5Taonani, akudza masiku, ati Yehova, akuti wolima adzapezana ndi wodula, ndi woponda mphesa adzapezana ndi wofetsa, ndi mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndi zitunda zonse zidzasungunuka. 14#Yes. 61.4; Yer. 30.3Ndipo ndidzabwezanso undende wa anthu anga Israele, ndipo adzamanganso mabwinja, ndi kukhala m'menemo; nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wake, nadzalima minda ndi kudya zipatso zake. 15#Yes. 60.21; Yow. 3.20Ndipo ndidzawaoka m'dziko mwao ndipo sadzazulidwanso m'dziko lao limene ndawapatsa, ati Yehova Mulungu wako.

Currently Selected:

AMOSI 9: BLPB2014

Highlight

Share

Compare

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in