YouVersion Logo
Search Icon

2 MBIRI 34

34
Yosiya achotsa chipembedzo cha mafano, nakonzanso Kachisi
1 # 2Maf. 22.1-2 Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi atatu mphambu chimodzi. 2Nachita zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira za Davide kholo lake, osapatuka kudzanja lamanja kapena kulamanzere. 3Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake; ndipo atakhala zaka khumi ndi chimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzichotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga. 4#2Maf. 23.4-6Ndipo anthu anagumula maguwa a nsembe a Abaala pamaso pake; nawalikha mafano a dzuwa anakwezeka pamwamba pao; naphwanya zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga; nazipera, naziwaza pamanda pa iwo amene adaziphera nsembe. 5Napsereza mafupa a ansembe pa maguwa a nsembe ao, nayeretsa Yuda ndi Yerusalemu. 6Nateronso m'midzi ya Manase, ndi Efuremu, ndi Simeoni, mpaka Nafutali, m'mabwinja mwao mozungulira. 7Nagumula maguwa a nsembe, naperapera zifanizo ndi mafano osema, nalikha mafano a dzuwa onse m'dziko lonse la Israele, nabwerera kunka ku Yerusalemu.
8 # 2Maf. 22.3-20 Atakhala mfumu tsono zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri, atayeretsa dziko ndi nyumbayi, anatuma Safani mwana wa Azaliya, ndi Maaseiya kazembe wa mudzi, ndi Yowa mwana wa Yehowahazi wolemba mbiri, akonze nyumba ya Yehova Mulungu wake. 9#2Maf. 12.4-16Ndipo anadza kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, napereka ndalama adabwera nazo kunyumba ya Mulungu, zimene Alevi osunga pakhomo adasonkhanitsa kuzilandira kudzanja la Manase ndi Efuremu, ndi kwa otsala onse a Israele, ndi kwa Yuda yense, ndi Benjamini, ndi kwa okhala m'Yerusalemu. 10Ndipo anazipereka m'dzanja la antchito oikidwa ayang'anire nyumba ya Yehova; ndi iwo anazipereka kwa antchito akuchita m'nyumba ya Yehova kukonza ndi kulimbitsa nyumbayi; 11anazipereka kwa amisiri a mitengo ndi omanga nyumba, agule miyala yosema, ndi mitengo ya mitanda yam'mwamba ndi yammunsi ya nyumbazi, adaziononga mafumu a Yuda. 12Ndipo amunawo anachita ntchitoyi mokhulupirika; ndi oikidwa awayang'anire ndiwo Yahati ndi Obadiya, Alevi, a ana a Merari; ndi Zekariya ndi Mesulamu, a ana a Akohati, kuifulumiza; ndi Alevi ena aliyense waluso la zoimbira. 13Anayang'aniranso osenza akatundu, nafulumiza onse akugwira ntchito ya utumiki uliwonse; ndi mwa Alevi munali alembi, ndi akapitao, ndi odikira.
Hilikiya apeza buku la chilamulo
14Ndipo pakutulutsa ndalama zimene adalowa nazo kunyumba ya Yehova, Hilikiya wansembe anapeza buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose. 15Ndipo Hilikiya anayankha nati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m'nyumba ya Yehova. Hilikiya napereka buku kwa Safani. 16Ndi Safani anamuka nalo buku kwa mfumu, nabwezeranso mau kwa mfumu, ndi kuti, Zonse mudazipereka kwa anyamata anu alikuzichita. 17Nakhuthula ndalama zinapezeka m'nyumba ya Yehova, nazipereka m'manja a akapitao ndi m'manja a antchito. 18Ndipo Safani mlembi anauza mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe anandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu. 19Ndipo kunali, atamva mfumu mau a chilamulo, anang'amba zovala zake. 20Mfumu niuza Hilikiya, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Abidoni mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti, 21Mukani, mundifunsire kwa Yehova, ine ndi otsala m'Israele ndi Yuda, za mau a m'buku lopezekalo; pakuti ukali wa Yehova atitsanulirawu ndi waukulu; popeza makolo athu sanasunge mau a Yehova kuchita monga mwa zonse zolembedwa m'bukumu.
Hulida aneneratu za kupasuka kwa Yerusalemu
22Namuka Hilikiya ndi iwo aja adawauza mfumu kwa Hulida mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasira wosunga zovala, amene anakhala m'Yerusalemu m'dera lachiwiri, nanena naye mwakuti. 23Ndipo iye ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine, 24Atero Yehova, Taonani, ndifikitsira malo ano ndi anthu okhala m'mwemo choipa, ndicho matemberero onse olembedwa m'buku adaliwerenga pamaso pa mfumu ya Yuda; 25chifukwa anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake ukali wanga utsanulidwa pamalo pano wosazimika. 26Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero kwa iye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kunena za mau udawamva, 27popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzichepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ake otsutsana nao malo ano, ndi okhala m'mwemo, ndi kudzichepetsa pamaso panga, ndi kung'amba zovala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova. 28Taona, ndidzakusonkhanitsa kumakolo ako, nudzaikidwa kumanda kwako mumtendere, ndi maso ako sadzapenya zoipa zonse ndidzafikitsira malo ano ndi okhala m'mwemo. Ndipo anambwezera mfumu mau.
Yosiya ndi anthu achitanso pangano ndi Mulungu
29 # 2Maf. 23.1-3 Pamenepo mfumu inatumiza anthu, nisonkhanitsa akuluakulu onse a Yuda ndi Yerusalemu. 30Nikwera mfumu kunyumba ya Yehova ndi amuna onse a m'Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu, ndi ansembe ndi Alevi, ndi anthu onse akulu ndi ang'ono; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a buku la chipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova. 31Ndipo mfumu inaimirira pokhala pake, nichita pangano pamaso pa Yehova, kuti adzayenda chotsata Yehova, ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, kuchita mau a chipangano olembedwa m'bukumu. 32Naimiritsapo onse okhala m'Yerusalemu ndi m'Benjamini. Ndipo okhala m'Yerusalemu anachita monga mwa chipangano cha Mulungu, Mulungu wa makolo ao. 33Yosiya nachotsa zonyansa zonse m'maiko onse okhala a ana a Israele, natumikiritsa onse opezeka m'Israele, inde kutumikira Yehova Mulungu wao. Masiku ake onse iwo sanapatuke kusamtsata Yehova Mulungu wa makolo ao.

Currently Selected:

2 MBIRI 34: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy