YouVersion Logo
Search Icon

2 MBIRI 32

32
Senakeribu agwera Yuda
1 # 2Maf. 18.13-19, 37; Yes. 36—37 Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Senakeribu mfumu ya Asiriya, nalowera Yuda, namangira midzi yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi. 2Ndipo pakuona Hezekiya kuti wadza Senakeribu, ndi kuti nkhope yake inalunjikitsa kuyambana nkhondo ndi Yerusalemu, 3anapangana ndi akulu ake ndi amphamvu ake, kutseka madzi a m'akasupe okhala kunja kwa mudzi; namthandiza iwo. 4Nasonkhana anthu ambiri, natseka akasupe onse, ndi mtsinje woyenda pakati pa dziko, ndi kuti, Angafike mafumu a Asiriya ndi kupeza madzi ambiri. 5#2Sam. 5.9; Yes. 22.9-10; 2Mbi. 25.23Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake, nalimbitsa Milo m'mudzi wa Davide, napanga zida ndi zikopa zochuluka. 6Naika akazembe a nkhondo alamulire anthu, nawasonkhanitsira kuli iye kubwalo la kuchipata cha mudzi, nanena nao motonthoza mtima wao ndi kuti, 7#Yos. 1.6-7, 9; 2Maf. 6.16; 2Mbi. 20.15Limbani, mulimbike mtima, musaopa kapena kutenga nkhawa pankhope pa mfumu ya Asiriya ndi aunyinji okhala naye; pakuti okhala nafe achuluka koposa okhala naye; 8#Yer. 17.5; Aro. 8.31pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anachirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.
9Pambuyo pake Senakeribu mfumu ya Asiriya, akali ku Lakisi ndi mphamvu yake yonse pamodzi naye, anatuma anyamata kwa Hezekiya mfumu ya Yuda, ndi kwa Ayuda onse okhala ku Yerusalemu, ndi kuti, 10Atero Senakeribu mfumu ya Asiriya, Mutama chiyani kuti mukhala m'linga m'Yerusalemu? 11Sakukopani Hezekiya, kuti akuperekeni mufe nayo njala ndi ludzu, ndi kuti, Yehova Mulungu wathu adzatilanditsa m'dzanja la mfumu ya Asiriya? 12Sanaichotse misanje yake ndi maguwa ake a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire kuguwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo? 13Simudziwa kodi chomwe ine ndi makolo anga tachitira anthu onse a m'maikomo? Kodi milungu ya mitundu ya anthu inakhoza konse kulanditsa dziko lao m'dzanja langa? 14Ndi uti mwa milungu yonse ya mitunduyi ya anthu, amene makolo anga anawaononga konse, unakhoza kulanditsa anthu ake m'dzanja mwanga? 15Ndipo tsono, asakunyengeni Hezekiya, ndi kukukopani motero, musamkhulupirira; pakuti palibe Mulungu wa mtundu uliwonse wa anthu, kapena ufumu uliwonse, unakhoza kulanditsa anthu ake m'dzanja mwanga; ndipo kodi Mulungu wanu adzakulanditsani inu m'dzanja langa? 16Ndipo anyamata ake anaonjeza kunena motsutsana ndi Yehova Mulungu, ndi mnyamata wake Hezekiya. 17#2Maf. 19.9, 12Analemberanso akalata a kunyoza Yehova Mulungu wa Israele, ndi kunena motsutsana ndi Iye, ndi kuti, Monga milungu ya mitundu ya anthu a m'maiko, imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja langa, momwemo Mulungu wa Hezekiya sadzalanditsa anthu ake m'dzanja mwanga. 18Ndipo anafuula ndi mau akulu m'chinenedwe cha Ayuda kwa anthu a m'Yerusalemu okhala palinga, kuwaopsa ndi kuwavuta, kuti alande mudziwu. 19Nanenera Mulungu wa Yerusalemu, monga umo amanenera milungu ya mitundu ya anthu a pa dziko lapansi, ndiyo ntchito ya manja a anthu. 20#2Maf. 19.2, 4, 15Ndipo Hezekiya mfumu, ndi Yesaya mneneri mwana wa Amozi, anapemphera pa ichi, nafuulira Kumwamba. 21#2Maf. 19.35-37Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, kuchigono cha mfumu ya Asiriya. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi kudziko lake. Ndipo atalowa m'nyumba ya mulungu wake, iwo otuluka m'matumbo mwake anamupha ndi lupanga pomwepo. 22Momwemo Yehova analanditsa Hezekiya ndi okhala m'Yerusalemu m'dzanja la Senakeribu mfumu ya Asiriya, ndi m'dzanja la onse ena, nawatsogolera monsemo. 23Ndipo ambiri anabwera nayo mitulo kwa Yehova ku Yerusalemu, ndi za mtengo wake, kwa Hezekiya mfumu ya Yuda; nakwezeka iye pamaso pa amitundu onse kuyambira pomwepo.
Nthenda ndi imfa ya Hezekiya
24 # 2Maf. 20.1-11; Yes. 38.1-8 Masiku omwe aja Hezekiya anadwala pafupi imfa; ndipo anapemphera kwa Yehova; ndi Iye ananena naye, nampatsa chizindikiro chodabwitsa. 25#Mas. 116.12Koma Hezekiya sanabwezere monga mwa chokoma anamchitira, pakuti mtima wake unakwezeka; chifukwa chake unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu. 26#1Maf. 21.27-28Koma Hezekiya anadzichepetsa m'kudzikuza kwa mtima wake, iye ndi okhala m'Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzera masiku a Hezekiya. 27Ndipo chuma ndi ulemu zinachulukira Hezekiya, nadzimangira iye zosungiramo siliva, ndi golide, ndi timiyala ta mtengo wake, ndi zonunkhira, ndi zikopa, ndi zipangizo zokoma zilizonse; 28ndi nyumba zosungiramo zipatso za tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zipinda za nyama iliyonse, ndi makola a zoweta. 29Nadzimangiranso midzi, nadzionera nkhosa ndi ng'ombe zochuluka; pakuti Mulungu adampatsa chuma chambirimbiri. 30#2Maf. 20.20Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire kumadzulo kwa mudzi wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo ntchito zake zonse. 31#2Maf. 20.12-19; Yes. 39.1-8Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babiloni, amene anatumiza kwa iye kufunsira za chodabwitsa chija chidachitika m'dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwake. 32#2Maf. 18.20; Yes. 36—39Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi ntchito zake zokoma, taonani, zilembedwa m'masomphenya a Yesaya mneneri mwana wa Amozi, ndi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele. 33Ndipo Hezekiya anagona ndi makolo ake, namuika polowerera kumanda a ana a Davide; ndi Ayuda onse ndi okhala m'Yerusalemu anamchitira ulemu pa imfa yake. Ndipo Manase mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.

Currently Selected:

2 MBIRI 32: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy