YouVersion Logo
Search Icon

2 MBIRI 14

14
Asa akantha Akusi
1Momwemo Abiya anagona ndi makolo ake, ndipo anamuika m'mudzi wa Davide; ndi Asa mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake; m'masiku ake dziko linaona bata zaka khumi. 2Ndipo Asa anachita chokoma ndi choyenera m'maso mwa Yehova Mulungu wake, 3nachotsa maguwa a nsembe achilendo, ndi misanje; naphwanya zoimiritsa zao, nalikha zifanizo zao, 4nauza Yuda afune Yehova Mulungu wa makolo ao, ndi kuchita chilamulo ndi chowauza Iye. 5Anachotsanso m'midzi yonse ya Yuda misanje, ndi zifanizo za dzuwa; ndi ufumuwo unachita bata pamaso pake. 6Ndipo anamanga midzi yamalinga m'Yuda; pakuti dziko linachita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa. 7Ndipo anati kwa Yuda, Timange midzi iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosavutika. 8Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a m'Yuda zikwi mazana atatu; ndi a m'Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu. 9Ndipo anawatulukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi chikwi chimodzi, ndi magaleta mazana atatu; nafika iye ku Maresa. 10Natuluka Asa pamaso pake, nanika nkhondoyi m'chigwa cha Zefati ku Maresa. 11Ndipo Asa anafuulira kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu; tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, tatulukira aunyinji awa m'dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakukanikeni. 12Ndipo Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Yuda, nathawa Akusi. 13Ndi Asa ndi anthu anali naye anawalondola mpaka ku Gerari, nagwa Akusi ambiri osalimbikanso mphamvu iwowa; pakuti anathyoledwa pamaso pa Yehova ndi ankhondo ake; ndipo anatenga zofunkha zambiri. 14#Gen. 35.5Ndipo anakantha midzi yonse pozungulira pake pa Gerari; pakuti mantha ochokera kwa Yehova anawagwera; ndipo anafunkha m'midzi monse, pakuti mudachuluka zofunkha m'menemo. 15Anakanthanso a m'mahema a ng'ombe, nalanda nkhosa zochuluka, ndi ngamira; nabwerera kunka ku Yerusalemu.

Currently Selected:

2 MBIRI 14: BLPB2014

Highlight

Share

Compare

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in