YouVersion Logo
Search Icon

1 SAMUELE 16

16
Samuele adzoza Davide akhale mfumu
1 # 1Sam. 10.1; Mas. 78.70 Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake. 2#1Sam. 9.12Ndipo Samuele anati, Ndikamuka bwanji? Saulo akachimva, adzandipha. Ndipo Yehova anati, Umuke nayo ng'ombe yaikazi, nunene kuti, Ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova. 3#Eks. 4.15; 1Sam. 9.16Ndipo uitane Yese abwere kunsembeko, ndipo Ine ndidzakusonyeza chimene uyenera kuchita; ndipo udzandidzozera iye amene ndidzakutchulira dzina lake. 4#2Maf. 9.22Ndipo Samuele anachita chimene Yehova ananena, nadza ku Betelehemu. Ndipo akulu a mudziwo anadza kukomana naye monthunthumira, nati, Mubwera ndi mtendere kodi? 5#Eks. 19.10Nati iye, Ndi mtendere umene; ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova; mudzipatule ndi kufika ndi ine kunsembeko. Ndipo iye anapatula Yese ndi ana ake, nawaitanira kunsembeko. 6Ndipo kunali, pakufika iwo, iye anayang'ana pa Eliyabu, nati, Zoonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pake. 7#1Maf. 8.39; Mas. 147.10-11; Yes. 55.8-9; Mat. 23.27-28Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima. 8Pamenepo Yese anaitana Abinadabu nampititsa pa Samuele. Ndipo iye adati, Koma uyunso Yehova sadamsankhe. 9Pamenepo Yese anapititsapo Sama. Ndipo anati, Koma uyunso Yehova sanamsankhe. 10Ndipo Yese anapititsapo ana ake amuna asanu ndi awiri. Koma Samuele anati kwa Yese, Yehova sanawasankhe awa. 11#2Sam. 7.8Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno. 12#1Sam. 9.17Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu. 13#1Sam. 10.10Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.
Davide atumikira Saulo
14 # Ower. 16.20; 1Sam. 18.10, 12; Mas. 51.11 Koma mzimu wa Yehova unamchokera Saulo, ndi mzimu woipa wochokera kwa Yehova unamvuta iye. 15Ndipo anyamata a Saulo ananena naye, Onani tsopano, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu ulikuvuta inu. 16Tsono inu mbuye wathu muuze anyamata anu, amene ali pamaso panu, kuti afune munthu wanthetemya wodziwa kuimba zeze; ndipo kudzakhala, pamene mzimu woipa wochokera kwa Mulungu uli pa inu, iyeyo adzaimba ndi dzanja lake, ndipo mudzakhala wolama. 17Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire tsono munthu wakudziwa kuimba bwino, nimubwere naye kwa ine. 18#1Sam. 18.14Ndipo mnyamata wake wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye. 19#1Sam. 16.11Chifukwa chake Saulo anatumiza mithenga kwa Yese, nati, Unditumizire Davide, mwana wako, amene ali kunkhosa. 20Ndipo Yese anatenga bulu namsenza mkate, ndi thumba la vinyo, ndi mwanawambuzi, nazitumiza kwa Saulo ndi Davide mwana wake. 21#Gen. 41.46Ndipo Davide anafika kwa Saulo, naima pamaso pake; ndipo iye anamkonda kwambiri, namsandutsa wonyamula zida zake. 22Ndipo Saulo anatumiza kwa Yese, nati, Ulole kuti Davide aime pamaso panga; pakuti ndamkomera mtima. 23Ndipo kunali kuti pamene mzimu woipawo wochokera kwa Mulungu unali pa Saulo, Davide anatenga zeze, naliza ndi dzanja lake; chomwecho Saulo anatsitsimuka, nakhala bwino, ndi mzimu woipa unamchokera iye.

Currently Selected:

1 SAMUELE 16: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy