YouVersion Logo
Search Icon

1 SAMUELE 15

15
Saulo alamulidwa aononge Amaleke
1Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Yehova ananditumiza ine kukudzozani mukhale mfumu ya anthu ake Aisraele; chifukwa chake tsono mumvere kunena kwa mau a Yehova. 2#Eks. 17.8, 14Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera chimene Amaleke anachitira Israele, umo anamlalira panjira, m'mene iye anakwera kutuluka m'Ejipito. 3Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamira ndi bulu.
4Ndipo Saulo anamemeza anthu, nawawerenga ku Telaimu, akuyenda pansi zikwi mazana awiri, ndi a kwa Yuda anthu zikwi khumi. 5Ndipo Saulo anafika kumudzi wa Amaleke, nalalira kuchigwa. 6#Num. 10.29, 32; Ower. 4.11Ndipo Saulo anauza Akeni kuti, Mukani, chokani mutsike kutuluka pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munachitira ana a Israele onse zabwino, pakufuma iwo ku Ejipito. Chomwecho Akeni anachoka pakati pa Aamaleke. 7Ndipo Saulo anakantha Aamaleke, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri, chili pandunji pa Ejipito. 8Namtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleke, naononga konsekonse anthu onse ndi lupanga lakuthwa. 9#1Sam. 15.3Koma Saulo ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng'ombe, ndi zonenepa zina, ndi anaankhosa, ndi zabwino zonse sadafuna kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konsekonse.
Samuele adzudzula Saulo pa kusamvera kwake
10Pamenepo mau a Yehova anafika kwa Samuele, nati, 11#1Sam. 15.35Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse. 12Ndipo Samuele analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Saulo; ndipo munthu anamuuza Samuele kuti, Saulo anafika ku Karimele, ndipo taonani, anaimika chikumbutso chake, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala. 13Ndipo Samuele anadza kwa Saulo; ndipo Saulo anati kwa iye, Yehova akudalitseni; ine ndinachita lamulo la Yehova. 14Ndipo Samuele anati, Koma tsono kulirako kwa nkhosa ndilikumva m'makutu anga, ndi kulirako kwa ng'ombe ndilikumva, nchiyani? 15#1Sam. 15.9, 21Ndipo Saulo anati, Anazitenga kwa Aamaleke; pakuti anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng'ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu; koma zina tinaziononga konsekonse. 16Pomwepo Samuele ananena ndi Saulo, Imani, ndidzakudziwitsani chimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani. 17#1Sam. 9.21Nati Samuele, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwa mutu wa mafuko a Israele? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israele. 18Ndipo Yehova anakutumani ulendo, kuti, Muka, nuononge konsekonse Aamaleke akuchita zoipawo, nuponyane nao kufikira utawatha. 19Chifukwa ninji tsono simunamvera mau a Yehova, koma munathamangira zowawanya, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova? 20#1Sam. 15.1Ndipo Saulo ananena ndi Samuele, Koma ndinamvera mau a Yehova, ndipo ndinayenda njira Yehova anandituma ine, ndipo ndinabwera naye Agagi mfumu ya Amaleke, ndi Aamaleke ndinawaononga konsekonse. 21#1Sam. 15.15Koma anthuwo anatengako zowawanya, nkhosa ndi ng'ombe, zoposa za zija tidayenera kuziononga, kuziphera nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala. 22#Mas. 50.8-9; Miy. 21.3; Yes. 1.11-17; Hos. 6.6; Aheb. 10.6-9Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo. 23#1Sam. 13.14Pakuti kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu. 24#Eks. 23.2; Yes. 51.12-13Ndipo Saulo anati kwa Samuele, Ndinachimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; chifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao. 25Chifukwa chake tsono, mukhululukire tchimo langa, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova. 26#1Sam. 15.23Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Ine sindibwerera nanu; pakuti munakaniza mau a Yehova, ndipo Yehova anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu ya Israele. 27Ndipo pakupotoloka Samuele kuti achoke, iye anagwira chilezi cha mwinjiro wake, ndipo chinang'ambika. 28#1Sam. 28.17-18Ndipo Samuele ananena naye, Yehova anang'amba ufumu wa Israele lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu. 29#Num. 23.19; Ezk. 24.14Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa. 30Pomwepo iye anati, Ndinachimwa, koma mundichitire ulemu tsopano pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Israele, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu. 31Chomwecho Samuele anabwerera natsata Saulo; ndi Saulo analambira Yehova.
32Ndipo Samuele anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleke. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira. 33#Num. 14.45Ndipo Samuele anati, Monga lupanga lako linachititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samuele anamdula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.
34Pamenepo Samuele ananka ku Rama; ndi Saulo anakwera kunka kunyumba yake ku Gibea wa Saulo. 35#1Sam. 15.11; 19.24Ndipo Samuele sanadzenso kudzaona Saulo kufikira tsiku la imfa yake; koma Samuele analira chifukwa cha Saulo; ndipo Yehova anali ndi chisoni kuti anamlonga Saulo mfumu ya Israele.

Currently Selected:

1 SAMUELE 15: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy