YouVersion Logo
Search Icon

1 AKORINTO 3

3
Chifukwa cha malekano ao
1 # 1Ako. 2.14-15 Ndipo ine, abale, sindinakhoza kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu. 2#Aheb. 5.12-13Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ai; pakuti simunachikhoza; ngakhale tsopano lino simuchikhoza; pakuti mulinso athupi; 3#1Ako. 1.11pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu? 4#1Ako. 1.12Pakuti pamene wina anena, Ine ndine wa Paulo; koma mnzake, Ndine wa Apolo; simuli anthu kodi? 5#1Ako. 4.1Ndipo Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa. 6#Mac. 18.4, 8, 11, 24; 1Ako. 15.10Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. 7#Mac. 18.4, 8, 11, 24; 1Ako. 15.10Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa. 8#Aro. 2.6Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha.
Akhristu ali nyumba ya Mulungu, Yesu ali maziko a nyumbayi
9 # 2Ako. 6.1; Aef. 2.20-22 Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu. 10#Aro. 15.20; 1Pet. 4.11Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo. 11#Aro. 11.33-34Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Khristu. 12Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golide, siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, udzu, dziputu, 13#1Ako. 4.5ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani. 14#1Ako. 4.5Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene anaimangako, adzalandira mphotho. 15Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto.
16 # 1Ako. 6.19 Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu? 17Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.
18 # Yes. 5.21 Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m'nthawi yino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru. 19#Yes. 5.21Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao; 20#Mas. 94.11ndiponso Ambuye azindikira zolingirira za anzeru, kuti zili zopanda pake. 21#2Ako. 4.15Chifukwa chake palibe mmodzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse nzanu; 22ngati Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena za makono ano, kapena zilinkudza; zonse ndi zanu; 23#Aro. 14.8koma inu ndinu a Khristu; ndi Khristu ndiye wa Mulungu.

Currently Selected:

1 AKORINTO 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in