Yesaya 39
39
Nthumwi Zochokera ku Babuloni
1Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani mfumu ya ku Babuloni anatumiza nthumwi kwa Hezekiya nawapatsira makalata ndi mphatso, pakuti anamva za kudwala kwake ndi kuti anachira. 2Hezekiya anawalandira mwasangala ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo siliva, golide, zokometsera zakudya, mafuta abwino kwambiri, zida zonse zankhondo ndiponso zonse zimene zinkapezeka mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse ka mʼnyumba yaufumu kapena mu ufumu wake onse kamene sanawaonetse.
3Tsono mneneri Yesaya anapita kwa mfumu Hezekiya ndipo anamufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani chiyani, ndipo anachokera kuti?”
Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”
4Mneneri anafunsanso kuti, “Kodi mʼnyumba yanu yaufumu anaonamo chiyani?”
Hezekiya anati, “Anaona chilichonse cha mʼnyumba yanga yaufumu. Palibe ndi chimodzi chomwe za mʼnyumba yosungiramo chuma changa chimene sindinawaonetse.”
5Pamenepo Yesaya anati kwa Hezekiya, “Imvani mawu a Yehova Wamphamvuzonse: 6Yehova akuti, nthawi idzafika ndithu pamene zonse za mʼnyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu anazisonkhanitsa mpaka lero lino, zidzatengedwa kupita nazo ku Babuloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe. 7Ndipo ena mwa ana anu, obala inu amene adzatengedwanso, ndipo adzawasandutsa adindo ofulidwa mʼnyumba ya mfumu ya ku Babuloni.”
8Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhula ndi abwino.” Ponena izi iye ankaganiza kuti, “Padzakhala mtendere ndi chitetezo masiku a moyo wanga onse.”
Currently Selected:
Yesaya 39: CCL
Highlight
Copy
Compare
Share
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.