Yesaya 20
20
Za Chilango cha Igupto ndi Kusi
1Mʼchaka chimene mkulu wankhondo wotumidwa ndi mfumu ya ku Asiriya, anabwera ku Asidodi ndi kuwuthira nkhondo ndi kuwulanda, 2nthawi imeneyo Yehova anawuza Yesaya mwana wa Amozi kuti, “Pita kavule chiguduli ndi nsapato zako.” Ndipo iye anaterodi, ankangoyenda wamaliseche ndiponso wopanda nsapato.
3Kenaka Yehova anati, “Monga momwe mtumiki wanga Yesaya wakhala akuyendera wamaliseche ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu ngati chizindikiro ndi chenjezo kwa dziko la Igupto ndi Kusi, 4momwemonso mfumu ya ku Asiriya idzatenga ukapolo anthu a ku Igupto ndi a ku Kusi, anyamata ndi okalamba. Iwo adzakhala amaliseche ndi opanda nsapato, matako ali pa mtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Igupto. 5Amene ankadalira Kusi, ndiponso amene ankadzitukumula chifukwa cha Igupto adzakhumudwa ndi kuchita manyazi. 6Tsiku limenelo anthu amene amakhala mʼmbali mwa nyanja adzati, ‘Taonani zomwe zawachitikira amene ife tinkawadalira, amene ife tinkathawirako kuti atithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya! Nanga ife tidzapulumuka bwanji?’ ”
Currently Selected:
Yesaya 20: CCL
Highlight
Copy
Compare
Share
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.