YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 2

2
Anzeru a kum'mawa
1 # Luk. 2.4-7 Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu, 2#Num. 24.17nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye. 3Ndipo Herode mfumuyo pakumva ichi anavutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye.
4 # Mala. 2.7 Ndipo pamene anasonkhanitsa ansembe aakulu onse ndi alembi a anthu, anafunsira iwo, Adzabadwira kuti Khristuyo?
5 # Mik. 5.2 Ndipo anamuuza iye, Mu Betelehemu wa Yudeya; chifukwa kunalembedwa kotere ndi mneneri, kuti,
6Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya,
sukhala konse wamng'onong'ono mwa akulu a Yudeya.
Pakuti Wotsogolera adzachokera mwa iwe,
amene adzaweta anthu anga Aisraele.
7Pomwepo Herode anawaitana Anzeruwo m'tseri, nafunsitsa iwo nthawi yake idaoneka nyenyeziyo. 8Nawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mau, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira Iye. 9Ndipo iwo, m'mene anamva mfumu, anamuka; ndipo onani, nyenyezi ija anaiona kum'mawa, inawatsogolera iwo, kufikira inadza nkuima pamwamba pomwe panali kamwanako. 10Ndipo iwo poona nyenyeziyo, anakondwera ndi kukondwera kwakukulu. 11#Mas. 72.10; Yes. 60.6Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure. 12#Mat. 1.20Ndipo iwo, pochenjezedwa m'kulota kuti asabwerere kwa Herode, anachoka kupita ku dziko lao panjira ina.
Athawira ku Ejipito
13Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko. 14Ndipo iye ananyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Ejipito; 15#Hos. 11.1nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti,
Ndinaitana Mwana wanga atuluke mu Ejipito.
Aphedwa ana mu Betelehemu
16Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo. 17#Yer. 31.15Pomwepo chinachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti,
18Mau anamveka mu Rama,
maliro ndi kuchema kwambiri;
Rakele wolira ana ake,
wosafuna kusangalatsidwa,
chifukwa palibe iwo.
Abwera kuchokera ku Ejipito
19Koma pakumwalira Herode, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera m'kulota kwa Yosefe mu Ejipito, 20nati, Tauka, nutenge kamwana ndi amake, nupite kudziko la Israele: chifukwa anafa uja wofuna moyo wake wa kamwanako. 21Ndipo anauka iye, natenga kamwana ndi amake, nalowa m'dziko la Israele. 22#Luk. 2.39Koma pakumva iye kuti Arkelao anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wake Herode, anachita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anachenjezedwa ndi Mulungu m'kulota, anamuka nalowa kudziko la Galileya, 23#Yoh. 1.45nadza nakhazikika m'mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.

Currently Selected:

MATEYU 2: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy