YouVersion Logo
Search Icon

YOHANE 18

18
Yesu mu Getsemani
1 # 2Sam. 15.23; Mat. 26.36 M'mene Yesu adanena izi, anatuluka ndi ophunzira ake, kunka tsidya lija la mtsinje wa Kidroni, kumene kunali munda, umene analowamo Iye ndi ophunzira ake.
Aperekedwa namangidwa
(Mat. 26.47-56; Mrk. 14.43-50; Luk. 22.47-53)
2 # Luk. 21.37 Koma Yudasinso amene akampereka Iye, anadziwa malowa; chifukwa Yesu akankako kawirikawiri ndi ophunzira ake. 3#Mat. 26.47Pamenepo Yudasi, m'mene adatenga gulu la asilikali ndi anyamata, kwa ansembe aakulu ndi Afarisi, anadza komweko ndi nyali ndi miuni ndi zida. 4Pamenepo Yesu, podziwa zonse zilinkudza pa Iye, anatuluka, nati kwa iwo, Mufuna yani? 5Anayankha Iye, Yesu Mnazarayo. Yesu ananena nao, Ndine. Koma Yudasi yemwe, wompereka Iye, anaima nao pamodzi. 6Ndipo m'mene anati kwa iwo, Ndine, anabwerera m'mbuyo, nagwa pansi. 7Pamenepo anawafunsanso, Mufuna yani? Koma iwo anati, Yesu Mnazarayo. 8Yesu anayankha, Nati, Ndine; chifukwa chake ngati mufuna Ine, lekani awa amuke; 9#Yoh. 17.12kuti akwaniridwe mau amene ati, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindinataye mmodzi. 10#Mat. 26.51Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, analisolola nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namsenga khutu lake lamanja. Koma dzina lake la kapoloyo ndiye Malkusi. 11#Mat. 20.22; 26.39, 42Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Longa lupanga m'chimake chake; chikho chimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ichi kodi?
Yesu kwa mkulu wa ansembe. Petro amkana
(Mat. 26.59-70; Mrk. 14.55-68; Luk. 22.55-57, 66-71)
12Ndipo khamulo ndi kapitao wamkulu, ndi anyamata a Ayuda anagwira Yesu nammanga Iye, 13#Luk. 3.2nayamba kupita naye kwa Anasi; pakuti anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chomwecho. 14#Yoh. 11.50Koma Kayafa anali uja wakulangiza Ayuda, kuti kuyenera munthu mmodzi afere anthu.
15 # Mat. 26.58 Koma Simoni Petro ndi wophunzira wina anatsata Yesu. Koma wophunzira ameneyo anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe, nalowa pamodzi ndi Yesu, m'bwalo la mkulu wa ansembe; 16#Mat. 26.69koma Petro anaima kukhomo kunja. Chifukwa chake wophunzira winayo amene anadziwika kwa mkulu wa ansembe, anatuluka nalankhula ndi wapakhomo, nalowetsa Petro. 17Pamenepo mdzakazi wapakhomoyo ananena kwa Petro, Kodi suli iwenso wa ophunzira a munthu uyu? Iyeyu ananena, Sindine. 18Koma akapolo anyamata analikuimirirako, atasonkha moto wamakala; pakuti kunali kuzizira; ndipo analikuotha moto; koma Petronso anali nao alikuimirira ndi kuotha moto.
19Ndipo mkulu wa ansembe anafunsa Yesu za ophunzira ake, ndi chiphunzitso chake. 20#Mat. 26.55Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi mu Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhule kanthu. 21Undifunsiranji Ine? Funsa iwo amene adamva chimene ndinalankhula nao; taona, amenewo adziwa chimene ndinanena Ine. 22#Yer. 20.2; Mac. 23.2Koma m'mene Iye adanena izi, mmodzi wa anyamata akuimirirako anapanda Yesu khofu, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa ansembe chomwecho? 23Yesu anayankha iye, Ngati ndalankhula choipa, chita umboni wa choipacho, koma ngati bwino, undipandiranji? 24Koma Anasi adamtumiza Iye womangidwa kwa Kayafa mkulu wa ansembe.
25 # Mat. 26.69, 71 Koma Simoni Petro analikuimirira ndi kuotha moto. Pomwepo anati kwa iye, Suli iwenso wa ophunzira ake kodi? Iyeyu anakana, nati, Sindine. 26Mmodzi wa akapolo a mkulu wa ansembe ndiye mbale wake uja amene Petro anamdula khutu, ananena, Ine sindinakuone iwe kodi m'munda pamodzi ndi Iye? 27#Mat. 26.74Pamenepo Petro anakananso; ndipo pomwepo analira tambala.
Yesu kwa Pilato
(Mat. 27.1-2, 11-31; Mrk. 15.1-20; Luk. 23.1-5, 13-25)
28 # Mat. 27.2; Mac. 10.28 Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska. 29Chifukwa chake Pilato anatulukira kunja kwa iwo, nati, Chifukwa chanji mwadza nacho cha munthu uyu? 30Anayankha nati kwa iye, Akadakhala wosachita zoipa uyu sitikadampereka Iye kwa inu. 31Ndipo Pilato anati kwa iwo, Mumtenge Iye inu, ndi kumweruza Iye monga mwa chilamulo chanu. Ayuda anati kwa iye, Tilibe ulamuliro wakupha munthu aliyense; 32#Mat. 20.18-19kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene akuti adzafa nayo.
33 # Mat. 27.11 Chifukwa chake Pilato analowanso mu Pretorio, naitana Yesu, nati kwa Iye, Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda kodi? 34Yesu anayankha, Kodi munena ichi mwa inu nokha, kapena ena anakuuzani za Ine? 35Pilato anayankha, Ndili ine Myuda kodi? Mtundu wako ndi ansembe aakulu anakupereka kwa ine; wachita chiyani? 36#Luk. 12.14Yesu anayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno. 37#1Yoh. 4.6Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mau anga. 38#Mat. 27.24Pilato ananena kwa Iye, Choonadi nchiyani? Ndipo pamene adanena ichi, anatulukiranso kwa Ayudawo, nanena nao, Ine sindipeza konse chifukwa mwa Iye. 39#Mat. 27.15Koma muli nao makhalidwe, akuti ndimamasulira inu mmodzi pa Paska; kodi mufuna tsono kuti ndimasulire inu mfumu ya Ayuda? 40#Luk. 23.18-19; Mac. 3.14Pomwepo anafuulanso, nanena, Si uyu, koma Barabasi. Koma Barabasi anali wachifwamba.

Currently Selected:

YOHANE 18: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy