1
Zek. 8:13
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
Inu mabanja a Yuda ndi Israele, kale munali chizindikiro cha matemberero pakati pa mitundu ina ya anthu. Koma tsopano ndidzakupulumutsani ndipo mudzakhala chizindikiro cha madalitso. Musaope, limbani mtima.
Compare
Explore Zek. 8:13
2
Zek. 8:16-17
Muzichita izi: muzikambirana zoona, muziweruza moona ndi mwamtendere m'mabwalo a milandu. Musamachitirane chiwembu, musamakonde kulumbira zonama, pakuti zonsezi ndimadana nazo.” Ndikutero Ine Chauta.
Explore Zek. 8:16-17