1
Mk. 1:35
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
M'mamaŵa ndithu, kusanache, Yesu adadzuka napita kumalo kosapitapita anthu. Kumeneko adakapemphera.
Compare
Explore Mk. 1:35
2
Mk. 1:15
Ankati, “Nthaŵi yakwana, Ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwinowu.”
Explore Mk. 1:15
3
Mk. 1:10-11
Potuluka m'madzimo, adangoona kuthambo kukutsekuka, ndipo Mzimu Woyera akutsika pa Iye ngati nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”
Explore Mk. 1:10-11
4
Mk. 1:8
Ine ndakubatizani ndi madzi, koma Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera.”
Explore Mk. 1:8
5
Mk. 1:17-18
Yesu adaŵauza kuti, “Inu, munditsate, ndikakusandutseni asodzi a anthu.” Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi.
Explore Mk. 1:17-18
6
Mk. 1:22
Zophunzitsa zake anthu zidaaŵagwira mtima kwambiri, chifukwa ankaphunzitsa moonetsa ulamuliro, kusiyana ndi m'mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo.
Explore Mk. 1:22