Tandiwonetsani ndalama yamsonkho.” Iwo adampatsadi ndalamayo. Pamenepo Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi nkhopeyi ndi ya yani, ndipo dzinali ndi la yani?” Iwo aja adati, “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.” Apo Yesu adaŵauza kuti, “Tsono perekani kwa Mfumu zake za Mfumuyo, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulungu.”