1
Mt. 18:20
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”
Compare
Explore Mt. 18:20
2
Mt. 18:19
“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani.
Explore Mt. 18:19
3
Mt. 18:2-3
Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao, ndipo adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mukapanda kusintha ndi kusanduka ngati ana, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.
Explore Mt. 18:2-3
4
Mt. 18:4
Nchifukwa chake munthu wodzichepetsa ngati mwana uyu, ameneyo ndiye wamkulu mu Ufumu wakumwamba.
Explore Mt. 18:4
5
Mt. 18:5
Ndipo aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene.”
Explore Mt. 18:5
6
Mt. 18:18
“Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mudzamanga pansi pano, chidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo chilichonse chimene mudzamasula pansi pano, chidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.
Explore Mt. 18:18
7
Mt. 18:35
“Inunsotu Atate anga akumwamba adzakuchitani zomwezo, aliyense mwa inu akapanda kukhululukira mbale wake ndi mtima wonse.”
Explore Mt. 18:35
8
Mt. 18:6
“Aliyense wochimwitsa ngakhale mmodzi mwa ana okhulupirira Ineŵa, ameneyo kukadakhala kwabwino koposa kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukammiza m'nyanja pozama.
Explore Mt. 18:6
9
Mt. 18:12
“Tsono mukuganiza bwanji? Munthu atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nkutayika, kodi sangasiye 99 zina zija m'phiri nkukafunafuna imodzi yotayikayo?
Explore Mt. 18:12