Mudzatenga pathupi, ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mudzamutcha dzina lake Yesu.
“Adzakhala wamkulu,
ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu Wopambanazonse.
Ambuye Mulungu adzamlonga ufumu wa kholo lake Davide,
ndipo adzakhala Mfumu ya Aisraele mpaka muyaya.
Ufumu wake sudzatha konse.”