Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kuchokera m'dziko la Ejipito wadziipsa; wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwanawang'ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.