Ndipo Mordekai analembera izi, natumiza akalata kwa Ayuda onse okhala m'maiko onse a mfumu Ahasuwero, a kufupi ndi a kutali, kuwalimbikitsira, asunge tsiku lakhumi ndi chinai, mwezi wa Adara, ndi tsiku lake lakhumi ndi chisanu lomwe, chaka ndi chaka, ndiwo masiku amene Ayuda anapumula pa adani ao; ndi mwezi wachisoni unawasandulikira wakukondwera, ndi wamaliro ukhale tsiku lokoma, awayese masiku amadyerero ndi akukondwera, akutumizirana magawo, ndi akupatsa zaufulu kwa osauka.