1
ESTERE 6:1-2
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
BLPB2014
Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu. Napeza mudalembedwa kuti Mordekai adawulula za Bigitana ndi Teresi, awiri a adindo a mfumu osunga pakhomo, amene adayesa kumthira manja mfumu Ahasuwero.
Compare
Explore ESTERE 6:1-2
2
ESTERE 6:6
Nalowa Hamani. Ndipo mfumu inati kwa iye, Kodi amchitire chiyani munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu? Ndipo Hamani anati mumtima mwake, Ndaniyo mfumu ikondwera kumchitira ulemu koposa ine?
Explore ESTERE 6:6
3
ESTERE 6:10
Pamenepo mfumu inati kwa Hamani, Fulumira, tenga chovala ndi kavalo monga umo wanenera, nuchitire chotero Mordekai Myudayo, wokhala pa chipata cha mfumu; kasasowepo kanthu ka zonse wazinena.
Explore ESTERE 6:10