1
1 AKORINTO 13:4-5
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
BLPB2014
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa
Compare
Explore 1 AKORINTO 13:4-5
2
1 AKORINTO 13:7
chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.
Explore 1 AKORINTO 13:7
3
1 AKORINTO 13:6
sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi
Explore 1 AKORINTO 13:6
4
1 AKORINTO 13:13
Ndipo tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.
Explore 1 AKORINTO 13:13
5
1 AKORINTO 13:8
Chikondi sichitha nthawi zonse, koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe.
Explore 1 AKORINTO 13:8
6
1 AKORINTO 13:1
Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.
Explore 1 AKORINTO 13:1
7
1 AKORINTO 13:2
Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.
Explore 1 AKORINTO 13:2
8
1 AKORINTO 13:3
Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m'moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ai.
Explore 1 AKORINTO 13:3
9
1 AKORINTO 13:11
Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.
Explore 1 AKORINTO 13:11
Home
Bible
Plans
Videos