1
Miyambo 19:21
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake, koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.
Compare
Explore Miyambo 19:21
2
Miyambo 19:17
Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.
Explore Miyambo 19:17
3
Miyambo 19:11
Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wosakwiya msanga; ulemerero wake uli posalabadira kuchitiridwa zoyipa.
Explore Miyambo 19:11
4
Miyambo 19:20
Mvera uphungu ndipo landira malangizo; pa mapeto pake udzakhala wanzeru.
Explore Miyambo 19:20
5
Miyambo 19:23
Kuopa Yehova kumabweretsa moyo; wotereyo amakhala mu mtendere; ndiye kuti choyipa sichidzamugwera.
Explore Miyambo 19:23
6
Miyambo 19:8
Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake. Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino.
Explore Miyambo 19:8
7
Miyambo 19:18
Langa mwana wako, chiyembekezo chikanalipo; ngati sutero udzawononga moyo wake.
Explore Miyambo 19:18
8
Miyambo 19:9
Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka.
Explore Miyambo 19:9