1
Mateyu 7:7
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
“Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani.
Compare
Explore Mateyu 7:7
2
Mateyu 7:8
Pakuti wopempha aliyense amalandira; ndi wofuna amapeza; ndipo iye amene agogoda, adzamutsekulira.
Explore Mateyu 7:8
3
Mateyu 7:24
“Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe.
Explore Mateyu 7:24
4
Mateyu 7:12
Nʼchifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu akuchitireni, yambani ndinu kuwachitira, pakuti izi ndi zimene malamulo ndi aneneri amaphunzitsa.
Explore Mateyu 7:12
5
Mateyu 7:14
Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo.
Explore Mateyu 7:14
6
Mateyu 7:13
“Lowani pa chipata chopapatiza. Pakuti chipata cholowera kuchiwonongeko nʼchachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo.
Explore Mateyu 7:13
7
Mateyu 7:11
Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha?
Explore Mateyu 7:11
8
Mateyu 7:1-2
“Musaweruze ena, kuti inunso mungadzaweruzidwe. Pakuti momwe inu muweruzira ena, inunso mudzaweruzidwa chimodzimodzi, muyeso umene muyesera ena inunso mudzayesedwa ndi womwewo.
Explore Mateyu 7:1-2
9
Mateyu 7:26
Koma aliyense amene amva mawu angawa ndi kusawachita ali ngati munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pa mchenga.
Explore Mateyu 7:26
10
Mateyu 7:3-4
“Chifukwa chiyani iwe uyangʼana kachitsotso ka mʼdiso la mʼbale wako koma susamalira chimtengo chili mʼdiso mwako? Kodi unganene bwanji kwa mʼbale wako kuti, ‘Ndikuchotse kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene nthawi zonse chimtengo uli nacho mʼdiso mwako?
Explore Mateyu 7:3-4
11
Mateyu 7:15-16
“Chenjerani nawo aneneri onyenga. Amabwera kwa inu atavala zikopa zankhosa, koma mʼkati mwawo ali mimbulu yolusa. Mudzawazindikira iwo ndi zipatso zawo. Kodi anthu amathyola mpesa pa mtengo wa minga, kapena nkhuyu pa nthula?
Explore Mateyu 7:15-16
12
Mateyu 7:17
Chimodzimodzinso mtengo wabwino umabala chipatso chabwino, koma mtengo woyipa umabala chipatso choyipa.
Explore Mateyu 7:17
13
Mateyu 7:18
Mtengo wabwino sungabale chipatso choyipa, ndi mtengo woyipa sungabale chipatso chabwino.
Explore Mateyu 7:18
14
Mateyu 7:19
Mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino umadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.
Explore Mateyu 7:19