1
Yeremiya 14:22
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Mwa milungu yachabechabe ya anthu a mitundu ina, kodi pali mulungu amene angagwetse mvula? Ife chikhulupiriro chathu chili pa Inu, popeza Inu nokha ndinu Yehova Mulungu wathu amene mukhoza kuchita zimenezi.
Compare
Explore Yeremiya 14:22
2
Yeremiya 14:7
Anthu akuti, “Ngakhale machimo athu akutitsutsa, koma Inu Yehova chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu. Pakuti kusakhulupirika kwathu nʼkwakukulu; ife takuchimwirani.
Explore Yeremiya 14:7
3
Yeremiya 14:20-21
Inu Yehova, ife tikuvomereza kuyipa kwathu ndiponso kulakwa kwa makolo athu; ndithu ife tinakuchimwiranidi. Musatikane kuopa kuti dzina lanu linganyozedwe; musanyoze mpando wanu waufumu waulemerero. Kumbukirani pangano lanu ndi ife ndipo musachiphwanye.
Explore Yeremiya 14:20-21