1
Ezekieli 12:28
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
“Choncho uwawuze kuti, ‘zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso; chilichonse chimene ndikunena chidzachitikadi. Ndikutero Ine Yehova.’ ”
Compare
Explore Ezekieli 12:28
2
Ezekieli 12:25
Koma Ine Ambuye ndidzayankhula chimene ndikufuna, ndipo chidzachitikadi, osachedwa ayi. Pakuti mʼmasiku anu omwe ano, inu anthu opanduka, ndidzakwaniritsa chilichonse chimene ndidzanena. Ndikutero Ine Yehova.’ ”
Explore Ezekieli 12:25
3
Ezekieli 12:2
“Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu owukira, iwowo maso openyera ali nawo, koma sakuona ndipo makutu omvera ali nawo, koma sakumva chifukwa choti ndi anthu owukira.
Explore Ezekieli 12:2