1
Eksodo 23:25-26
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Muzipembedza Yehova Mulungu wanu ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi ndiponso ndidzachotsa nthenda pakati panu. Palibe mkazi amene adzapite padera kapena kukhala wosabereka mʼdziko mwanu. Ndidzakupatsani moyo wautali.
Compare
Explore Eksodo 23:25-26
2
Eksodo 23:20
“Taona Ine ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu kuti akutetezeni mʼnjiramo ndi kukakufikitsani ku malo amene ndakonza.
Explore Eksodo 23:20
3
Eksodo 23:22
Ngati mudzamvera iyeyu ndi kuchita zonse zimene Ine ndikunena, Ine ndidzakhala mdani wa adani anu ndipo ndidzatsutsana ndi onse otsutsana nanu.
Explore Eksodo 23:22
4
Eksodo 23:2-3
“Usatsate gulu la anthu ndi kuchita choyipa. Pamene ukupereka umboni mʼbwalo lamilandu, usakhotetse mlandu chifukwa chofuna kukondweretsa anthu ambiri. Ndipo poweruza mlandu wa munthu wosauka usamukondere.
Explore Eksodo 23:2-3
5
Eksodo 23:1
“Usafalitse mbiri yabodza. Usathandize munthu wolakwa pomuchitira umboni wonama.
Explore Eksodo 23:1