Ine ndinaonanso chinthu china pansi pano:
opambana pa kuthamanga si aliwiro,
kapena opambana pa nkhondo si amphamvu,
ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru,
kapena okhala ndi chuma si odziwa zambiri,
kapena okomeredwa mtima si ophunzira;
koma mwayi umangowagwera onsewa pa nthawi yake.