1
Mlaliki 1:18
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Pakuti nzeru zochuluka zimabweretsa chisoni chochulukanso: chidziwitso chochuluka, zowawa zochulukanso.
Compare
Explore Mlaliki 1:18
2
Mlaliki 1:9
Zomwe zinalipo kale zidzakhalaponso, zomwe zinachitika kale zidzachitikanso. Ndiye kuti chatsopano palibiretu pansi pano.
Explore Mlaliki 1:9
3
Mlaliki 1:8
Zinthu zonse ndi zotopetsa, kutopetsa kwake ndi kosaneneka. Maso satopa ndi kuona kapena khutu kukwaniritsidwa ndi kumva.
Explore Mlaliki 1:8
4
Mlaliki 1:2-3
“Zopandapake! Zopandapake!” atero Mlaliki. “Zopandapake kotheratu! Zopandapake.” Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zake zonse zimene amasautsidwa nazo pansi pano?
Explore Mlaliki 1:2-3
5
Mlaliki 1:14
Ine ndaona zinthu zonse zochitika pansi pano; zinthu zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
Explore Mlaliki 1:14
6
Mlaliki 1:4
Mibado imabwera ndipo mibado imapita, koma dziko lapansi limakhalapobe nthawi zonse.
Explore Mlaliki 1:4
7
Mlaliki 1:11
Anthu akale sakumbukiridwa, ngakhale amene adzabwera mʼtsogolomu sadzakumbukiridwa ndi iwo amene adzabwere pambuyo pawo.
Explore Mlaliki 1:11
8
Mlaliki 1:17
Ndipo ndinadzipereka kuti ndithe kumvetsa kuti nzeru nʼchiyani, misala nʼchiyani, uchitsiru nʼchiyani, koma ndinazindikira ichi, kuti kuteronso nʼkungodzivuta chabe.
Explore Mlaliki 1:17