Maluko 4
4
Chifani cha mundhu wovyala mbewu
Matayo 13:1-9; Luka 8:4-8
1Yesu wadayambhanjho kuyaluza mmbhepete mwa nyanja ya Galilaya. Gulu lalikulu la wandhu lidamzungulila, mbaka wadakwela mboti ni kukhala mmenemo kuti wandhu saadamzenga. Wandhu wonjhe adakhala mmbhepete mwa nyanja. 2Wadaayaluza vindhu vambili mwa vifani, ni mmayaluzo yake wamakambila, 3“Vechelani! Wovyala wadapita kumijha mbewu. 4Yapo wamamijha mbewu, zina zidagwela panjila, mbalami zidajha ni kuzidya. 5Zina zidagwela pamwala yapo palibe dothi lambili, zidamela chisanga ndande dothi lidali lochepa. 6Jhuwa yapo lidatuluka, lidaphyeleza mimela, pakuti mizo yake siidapite panjhi. 7Zina zidagwela pa minga, nazo zijha minga zidakula ni kuzizinga zijha mimela, ni siidabale njele yaliyonjhe. 8Zina zidagwela pa dothi la chaila, zidamela, ni zidakula ni kubala, imojhi idabala njele selasini, ina adabala njele sitini, ni ina adabala njele miya.” 9Ndiipo Yesu wadakambila, “Mchate icho mkambidwa!”
Ndande ya Yesu kuyaluza kwa vifani
Matayo 13:10-17; Luka 8:9-10
10Yesu yapo wadali yokha, wandhu wina adamzungulila Yesu ni anyiwajha oyaluzidwa khumi ni awili, adamfunjha mate ya vifani vimenevo. 11Yesu wadaakambila, “Anyimwe mwapachidwa mwawi wojhiwa visisi va Ufumu wa Mnungu, nambho anyiwajha ali kubwalo siavele nghani zonjhe kwa chifani, 12kuti,
‘Apenye, nambho siadaona.
Avele, nambho sazindikila.
Adakajhiwa, adakambwelela Mnungu,
Nayo wadakalekelela machimo yao.’”
Yesu wafotokoza vifani cha wovyala mbewu
Matayo 13:18-23; Luka 8:11-15
13Ndiipo Yesu wadaafunjha, “Bwanji, anyiimwe simdajhiwe mate ya chifani ichi? Chipano simjhiwe bwanji vifani vina? 14Wovyala wavyala Mawu la Mnungu. 15Wandhu wina alingana ni mbewu izo zagwela mmbepete mwa njila, yapo avela mawu la Mnungu, Satana wakujha ni kulitenga lijha mawu la Mnungu lidavyalidwa mkati mwawo. 16Wandhu wina alingana ni zijha mbewu zidagwela pa myala, yapo avela mawu la Mnungu alilandila kwa chikondwelo. 17Nambho augwila uthenga kwa ndhawi yochepa, ndande ali ngati mimela iyo ilibe mizo. Yapo avutika ni kuchauchika ndande ya Mawu la Mnungu, pamenepo akufa mtima. 18Wandhu wina alingana ni mbewu izo zidagwela paminga, anyiiwo alivela Mawu la Mnungu, 19nambho mavuto ya jhiko lino, ni kukhumbila chuma ni kukhumbila kupata vindhu vambili, vaalowa mkati mwawo, ni kwachita saadalipotela njhito Mawu la Mnungu. 20Wandhu wina alingana ni mbewu izo zidagwela pa ndhaka yachayila, yapo avela Mawu la Mnungu, ni alikhulupilila ni kulipotela njhito, ngati umo mbewu imojhi idabala njele selasini, ni ina njele sitini ni ina njele miya mojha.”
Chifani cha nyali iyo yavinikilidwa
Luka 8:16-18
21Yesu wadayendekela kwaakambila, “Bwanji, mundhu wakhoza kukweleza nyali mkati ni kuvinikila mphika, kapina kunjhi kwa chitala? Notho, aika pamalo yapo aika nyali. 22Chimwecho, chindhu chalichonjhe icho chabisibwa sichioneke ni chilichonjhe icho chavinikilidwa sichivunukulidwe. 23Mchate icho mkambidwa!”
24Chinchijha wadaakambila, “Mkhale maso ni yayo muyavela. Chimchijha umo mujhichocha kuvechela mawu nde chimwecho Mnungu siwakuchite ulijhiwe mawu kupunda. 25Mundhu uyo wavechela mawu la Mnungu ni kulijhiwa, Mnungu siwamthangatile ni kumchita walijhiwe kupunda. Ngati mundhu siwavechela mawu la Mnungu, ata mawu laling'ono la Mnungu ilo walijhiwa siwalandidwe.”
Chifani cha mbewu iyo imela
26Yesu wadaendekela kukamba, “Ufumu wa Mnungu ulingati chimwechi. Mundhu mmojhi wadamijha mbewu mmunda. 27Usiku wamagona, ni usana wakhala maso, mbeu zimela ni kukula popande iye siwajhiwa icho chichitika. 28Idali chimwecho ndande dothi lene liikhozecha mmela kukula, ni kubala vokolola. 29Mapila yapo yakhwima, yujha mundhu wadula ni chisenga chake, pakuti nyengo ya vokolola yakwana.”
Chifani cha mbewu ya haladali
Matayo 13:31-32,34; Luka 13:18-19
30Yesu wadafunjhanjho, “Bwanji, Ufumu wa Mnungu ulingana ni chiyani? Bwanji, tiufotokoze kwa chifani chanji? 31Ulingana ni mbewu yaing'ono ya haladali iyo ili yaing'ono kupitilila mbewu zonjhe pajhiko. 32Nambho ikavyalidwa, imela ni kukhala mtengo waukulu kupitilila mitengo yonjhe ya mmunda, ni ndhawi zake zikhala zazikulu, ni mbalame zikhoza kumanga visa mndhawi zake”
33Yesu wadauzila wandhu uthenga wake kwa vifani vina vambili va mtundu umeneo, ni wadakambila ngati umo adakhozela kujhiwa. 34Yesu siwadakambe nao chindhu chilichonjhe popande chifani, nambho yapo wadali ni oyaluzidwa wakepe, wadaakambila kila chindhu.
Yesu waunyindila mwela
Matayo 8:23-27; Luka 8:22-25
35Siku limwelo ujhulo, Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, “Tiyomboke chijya la nyanja Galilaya.” 36Adausiya ujha msonghano wa wandhu, oyaluzidwa adapita pamojhi ni iye mboti mujha wadalimo Yesu, adachoka nayo. Chimwechonjo kudali ni maboti ina yambili pamalo pamenepo. 37Papajha mwela waukulu udachokela, ni mafunde yadalibula lijha boti wadalimo Yesu mbaka lidayamba kujhala majhi. 38Yesu wadali kumbuyo kwa lijha boti wadatogonela philo, oyaluzidwa wake adamuucha ni kumkambila, “Oyaluza, simganizila kuti ife titobila?”
39Ndiipo Yesu wadauka ni kuunyindila mwela, “Khala chete!” Pampajha mwela udasiya ni nyanja idagona.
40Chimwecho Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, “Ndande yanji muopa? Bwanji, mkali mlibe chikulupililo?”
41Oyaluzidwa wake adaopa kupunda, adafunjhana, “Mundhu wa mtundu wanji uyu mbaka mwela umvela?”
Currently Selected:
Maluko 4: NTNYBL2025
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: