YouVersion Logo
Search Icon

Vichito 5

5
Ananiya ni Safila atonyenga
1Kudali mundhu uyo wamatanidwa Ananiya pamojhi ni mkazake uyo watanidwa Safila adagulicha munda wao uwo adalinao. 2Nambho Ananiya ni mkazake adagwilizana kubisa ndalama yakumojhi, ni kupeleka ndalama izo zidakhalila kwa atumwi. 3Petulo wadaakambila, “Ananiya, ndande yanji wamulola Satana wakulamulile ni kukuchita umunyenge Mzimu Woyela kwa kubisa ndalama zakumojhi ya izo udagulicha munda? 4Yapo udali ukali osaghuliche munda udali wako, niyapo udaghulicha ndalama zidalinjho zako ni udakakhoza kutumila ngati umo ufunila iwe. Ndande yanji udaganiza kuchita chimwechi mumtima mwako? Siudamnyenge mundhu, nambho wamnyenga Mnungu.” 5Ananiya yapo wadavela chimwecho, wadagwa panjhi ni kumwalila. Mandha yayakulu yadaapata wandhu wonjhe yawo adavela nghani izo zidachokela. 6Anyamata adalowa ni kumvinikila sanda thupi lake, adamtulucha kubwalo ni kumzika. 7Yapo zidatha saa zitatu, mkazake Ananiya wadalowa, osajhiwa icho chachokela. 8Petulo wadamkambila, “Nikambile, bwanji izi nde ndalama zonjhe izo mudagulicha munda wanu?” Iye wadayangha, “Yetu tidagulicha kwa ndalama zimenezo.” 9Petulo wadamfunjha, “Ndandeyanji muvomelezana kumuyesa Mzimu wa Ambuye? Wandhu yawo amzika mmunako sazino ali pachicheko, nawenjho saapite kukuzika.” 10Ndhawi imweyo Safila wadagwa panjhi ni kumwalila ni mmyendo mwa Petulo. Anyamata wawajha adajha ni adakomana wathokufa, adamtenga ni kupita kumzika pambhepete pa chiliza cha mmunake. 11Gulu lonjhe, pamojhi ni wandhu wina yawo adavela nghani izi adagwilidwa ni mandha.
Atumwi alamicha wandhu ambili
12Atumwi adachita vodabwicha ni vozizwicha vambili pakati pa wandhu. Wandhu adamkhulupilila Yesu wonjhe adakomana kwa pamojhi pa Nyumba ya Amnungu pamalo yapo patanidwa khumbi la Solomoni. 13Padalibe mundhu mwina waliyonjhe uyo siwamdakhulupilile Yesu wadayesa kulunjana nawo. Ata chimwecho, wandhu wina yawo sadamkhulupilile Yesu wadalemekeza. 14Nambho chiwelengo cha wandhu yawo adamkhulupilila Ambuye, amachuluka kupunda wachimuna ni waachikazi. 15Wandhu amajhanawo wodwala ni kwaagoneka pamagodolo ni muvithanda mnjila, kuti ngati ikakhozeka, yapo Petulo siwajhipita, chitunjhi chake chigafye wina wao kuti alame. 16Gulu la wandhu lidajha kuchokela mmijhi yozungulila Yelusalemu, niajhanawo wodwala wawo ni yawo adazamwa ni viwanda, ni vonjhe adalamichidwa.
Atumwi avutichidwa
17Ndiipo mjhukulu wa Mkulu ni wonjhe yawo adali pamojhi ni iye, yawo adali agulu la Asadukayo, wadaonela njhanje atumwi, ni kuganiza kwaachitila voipa. 18Wadaagwila atumwi ni kwaaika mndende. 19Nambho usiku mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadachekula vicheko va ndende ni kwaatulucha kubwalo, niwakamba, 20“Pitani mkaime pa nyumba ya Mnungu, mkakambile wandhu mawu yonjhe ya umoyo uno wolunjana ni Yesu.” 21Atumwi wajha yapo adavela yaya, adapita Mnyumba ya Mnungu umawamawa nikuyamba kuyaluza wandhu
Wamkulu wa Ajhukulu ni achanjake yapo adafika, adatana pamojhi msonghano wa bwalo lalikulu la milandu la azee wa a Izilaeli, ni adaatuma wandhu mndende wapelekele wajha atumwi.
22Nambho alonda wajha yapo adafika kundende, siadampeze atumwi ata mmojhi. Chimwecho adabwelela kwa azee a bwalo la milandu kwaakambila ivo vachitika, 23adakamba, “Yapo ife tidafika pa ndende, tidapheza vicheko vonjhe vachekedwa ni alonda wonjhe adalipo, nambho yapo tidachekula chicheko, sitidamphezemo mundhu ata mmojhi.” 24Wamkulu wa alonda wa nyumba ya Mnungu ni wamkulu wa ajhembe yapo adavela chimwechi, adagwilidwa ni mandha kupunda, sadajhiwe icho chidachokela. 25Ndiipo mundhu mmojhi wadajha ni kwaakambila, “Vechalani, wandhu wajha mudaika mndende atuluka ali pa Nyumba ya Mnungu atoyaluza wandhu!” 26Ndiipo wamkulu wa Nyumba ya Mnungu wadachoka pamojhi ni asikali ni kwaabweza atumwi wajha mndende. Nambho siwadagwile kwa mbhavu ndande adaopa angamenyedwe myala ni wandhu.
27Basi yapo adaabweza atumwi wajha mndende, wadaalamula kuima pabwalo la milandu. Mjhukulu wamkulu wadaafunjha, 28“Tidakukanizani kwa mbhavu kuti simudayaluza kupitila jhina la Yesu, nambho penyani icho muchichita! Mwaeneza mayaluzo yanu mujhiko lonjhe la Yelusalemu, ni kufuna kutipacha milandu ya kumpha mundhu mmeneyo.”
29Pamenepo Petulo pamojhi ni atumwi wina adayangha, “Ifunika timvele Mnungu kusiyana ni kwaavela wandhu! 30Ayiimwe mudampha Yesu pakumpachika pamtanda, nambho Mnungu wa azee wathu wadamuhyukicha. 31Uyu nde uyo Mnungu wadampacha ulemu ni kumuika kujhanja lake la kwene kuti wakhale mchogoleli ni Muomboli, kuti waapache wandhu a Izilaeli mwawi wolapa ni kulekeleledwa machimo yao. 32Ife ni amboni a nghani zimenezo, chinchijha ata Mzimu Woyela uyo Mnungu waapacha wandhu wajha amvela wachimikiza chindhu chimenecho.”
33Azee wonjhe a bwalo yapo adavela chimwecho, adakwiiya kupunda mbaka amafuna kuti atumwi aphedwe. 34Nambho Mfalisayo mmojhi, jhina lake Gamalieli, uyo wadali oyaluza wa thauko ni wadali wolemekezedwa kupunda ni wandhu wonjhe, wadaima pakati pa bwalo. Iye wadalamula atumwi atuluchidwe kubwalo kwa ndhawi yochepa, 35ndiipo wadalikambila bwalo la azee, “Anyiimwe a Izilaeli anjanga, mjhipenyelele ni yayo mufuna kwaachitila wandhu anyiyawa. 36Kale wadajha mundhu mmojhi uyo watanidwa Seuda, uyo wadajhichita kuti iye ni mundhu wojhiwika, wadaapata wochatila ngati miya zinayi. Nambho wadaphedwa, ni ochatila wake wonjhe adamwazika ni nghani yake idathela pamenepo. 37Pambuyo pake wadachokela Yuda wa ku Galilaya ndhawi ya wandhu kuwelengedwa, wadaaguza wandhu ambili kwaiye, nayo wadapedwa, ni wandhu wonjhe yawo adamchata adamwazika. 38Chipano nikuonyani, mwaasiye wandhu anyiyawa, ngati ganizo lao kapina njhito iyo achita yachokela kwa wandhu, siite yene. 39Nambho ngati njhito izi zachokela kwa Mnungu, simukhoza kwaakaniza wandhu anyiyawa, mmalo mwake simukhale nimmenyana ni Mnungu.”
Wandhu wonjhe adavomelezana ni Gamalieli.
40Wandhu wajha adavela ivo wadakamba Gamalieli. Wadaatana atumwi wajha mkati, adalamula kuti akwapulidwe mikwapulo, ndiipo wadalamula kuti sadayaluzanjho kwa jhina la Yesu, ndiipo adaasiya ajhipita. 41Atumwi wajha adatuluka ku bwalo la milandu mujha, uku niakondwa, pakuti Mnungu wadaachita alemekezeke, kwa kwaasiya alenge njhoni ndande ya jhina la Yesu. 42Kila siku atumwi adaendekele kuyaluza ni kulalika uthenga wabwino pa Nyumba ya Mnungu ni mnyumba za wandhu kuti Yesu nde Kilisito.

Currently Selected:

Vichito 5: NTNYBL2025

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in