Mt. 28:12-15
Mt. 28:12-15 BLY-DC
Tsono akulu a ansembe aja ndi akulu a Ayuda adasonkhana napangana nzeru. Adapatsa alonda aja ndalama zambiri, naŵauza kuti, “Muziti, ‘Ophunzira ake anabwera usiku nkuba mtembo wake ife tili m'tulo.’ Choncho bwanamkubwa akamva zimenezi, ife tidzamkhazika mtima pansi, ndipo sipadzakhala kanthu kokuvutani.” Alonda aja atalandira ndalama zija, adachitadi monga momwe adaaŵauzira. Motero mbiri imeneyi idawanda pakati pa Ayuda mpaka lero lino.





