Mt. 27
27
Yesu ku bwalo la Pilato
(Mk. 15.1; Lk. 23.1-2; Yoh. 18.28-32)
1M'maŵa kutacha, akulu onse a ansembe ndi akulu a Ayuda adapanga upo kuti aphe Yesu. 2Adammanga, napita naye kwa Pilato, bwanamkubwa.
Za imfa ya Yudasi
(Ntc. 1.18-19)
3 #
Ntc. 1.18, 19 Pamene Yudasi, wopereka Yesu kwa adani ake uja, adaona kuti Yesu mlandu wamuipira, nthumanzi idamugwira. Tsono adakaŵabwezera akulu a ansembe ndi akulu a Ayudawo ndalama makumi atatu zasiliva zija. 4Adati, “Ndidachimwa pakupereka munthu wosalakwa kuti aphedwe.” Koma iwo adati, “Ife tilibe nazo kanthu. Izo nzako.” 5Yudasi adakaziponya ndalamazo m'Nyumba ya Mulungu nachokapo, kenaka nkukadzikhweza.
6Akulu a ansembe aja adatola ndalamazo nati, “Malamulo athu satilola kuika ndalamazi m'bokosi la chuma cha m'Nyumba ya Mulungu, popeza kuti ndi za magazi.” 7Choncho adapangana kuti ndalamazo agulire munda wa mmisiri wa mbiya, kuti ukhale manda a alendo. 8Nchifukwa chake mpaka lero mundawo umatchedwa “Munda wa Magazi.”
9 #
Zek. 11.12, 13 Motero zidapherezera zimene mneneri Yeremiya adaanena kuti, “Adatenga ndalama zija makumi atatu, mtengo wake umene Aisraele adaagamula, 10nagulira munda wa mmisiri wa mbiya, monga momwe Ambuye adaandilamulira.”
Pilato afunsa Yesu mafunso
(Mk. 15.2-5; Lk. 23.3-5; Yoh. 18.33-38)
11Tsono Yesu adaimirira pamaso pa bwanamkubwa. Iyeyo adamufunsa kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adati, “Mwanena nokha.” 12Koma pamene akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda aja ankamuneneza, Yesu sadayankhepo kanthu. 13Apo Pilato adamufunsa kuti, “Kodi sukumva zonse akukunenezazi?” 14Koma Yesu sadamuyankhe kanthu, kotero kuti bwanamkubwa uja adadabwa kwambiri.
Pilato agamula kuti Yesu aphedwe
(Mk. 15.6-15; Lk. 23.13-25; Yoh. 18.39—19.16)
15Pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska, bwanamkubwa ankaŵamasulira anthu mkaidi mmodzi, yemwe iwo ankafuna. 16Pa nthaŵi imeneyo panali mkaidi wina wodziŵika, dzina lake Barabasi. 17Tsono anthu atasonkhana, Pilato adaŵafunsa kuti, “Mukufuna kuti ndikumasulireni uti, Barabasi kapena Yesu, wotchedwa Khristu?” 18Adaatero chifukwa adaadziŵa kuti Yesuyo anthuwo angodzampereka chifukwa cha kaduka chabe.
19Pilato ali pa mpando woweruzira milandu, mkazi wake adamtumizira mau. Adati, “Musaloŵerepo pa nkhani ya munthu wolungamayo. Inetu maloto andivuta kwambiri usiku chifukwa cha Iyeyo.”
20Akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda adayamba kukakamiza anthu kupempha Pilato kuti amasule Barabasi, ndipo kuti Yesu aphedwe. 21Tsono bwanamkubwa uja adaŵafunsa kuti, “Mukufuna kuti ndikumasulireni uti mwa aŵiriŵa?” Anthu aja adati, “Barabasi.” 22Pilato adaŵafunsa kuti, “Nanga tsono ndichite naye chiyani Yesu, wotchedwa Khristuyu?” Anthu onse aja adati, “Apachikidwe pa mtanda!” 23Pilato adaŵafunsanso kuti, “Adalakwanji?” Koma anthu aja adafuula koposa kuti, “Apachikidwe pa mtanda!” 24#Deut. 21.6-9Pilato adaona kuti sakuphulapo kanthu, ndipo kuti anthu ali pafupi kuchita chipwirikiti. Choncho adaitanitsa madzi, nkusamba m'manja pamaso pa anthu onse, nanena kuti, “Ine ndiye ndilibe kanthu pa imfa ya munthuyu. Izo nzanu.” 25Anthu onse aja adati, “Imfayo mlandu wake ugwere ife ndi ana athu.” 26Apo Pilato adaŵamasulira Barabasi, nalamula kuti Yesu akwapulidwe. Pambuyo pake adampereka kuti akampachike pa mtanda.
Asilikali achita Yesu chipongwe
(Mk. 15.16-20; Yoh. 19.2-3)
27Pamenepo asilikali a bwanamkubwa adatenga Yesu nakaloŵa naye kunyumba kwa bwanamkubwa. Adasonkhanitsa gulu lonse la asilikali anzao nazinga Yesu. 28Adamuvula zovala zake, namuveka chovala chofiira. 29Adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake, ndipo adamgwiritsa ndodo m'dzanja lake lamanja. Kenaka adayamba kumgwadira, namaseŵera naye mwachipongwe nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.” 30Adamthira malovu, natenga ndodo ija nkumamumenya nayo m'mutu. 31Ataseŵera naye mwachipongwe choncho, adamuvula chovala chija namuvekanso zovala zake. Kenaka adamtenga, nkupita naye kuti akampachike pa mtanda.
Yesu apachikidwa pa mtanda
(Mk. 15.23-32; Lk. 23.26-43; Yoh. 19.17-27)
32Pamene ankatuluka mumzindamo, adakumana ndi munthu wina, dzina lake Simoni, wa ku Kirene. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu. 33Ndipo adafika ku malo otchedwa Gologota, (ndiye kuti “Malo a Chibade cha Mutu.”) 34#Mas. 69.21Kumeneko adapatsa Yesu vinyo wosanganiza ndi ndulu kuti amwe. Koma atalaŵa, adakana kumwa.
35 #
Mas. 22.18
Atampachika pa mtanda, adagaŵana zovala zake pakuchita maere. 36Kenaka adakhala pansi namamlonda. 37Pamwamba pa mutu wake adaalembapo mau osonyeza mlandu womuphera, akuti, “Uyu ndi Yesu, Mfumu ya Ayuda.” 38Adapachikanso pa mitanda zigaŵenga ziŵiri, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere.
39 #
Mas. 22.7; 109.25; Mphu. 12.17, 18; 13.7 Anthu amene ankadutsa pamenepo, ankamunyodola nkumapukusa mitu. 40#Mt. 26.61; Yoh. 2.19 Ankanena kuti, “Iwe, suja unkati, ‘Ndidzapasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu?’ Ngati ndiwedi Mwana wa Mulungu tadzipulumutsatu nkutsika pamtandapo.” 41Nawonso akulu a ansembe pamodzi ndi aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda ankamuseka. Ankati, 42“Adapulumutsa anthu ena, koma akulephera kudzipulumutsa Iye mwini. Si Mfumu ya Aisraele nanga? Atsiketu tsopano pamtandapo kuti timkhulupirire. 43#Mas. 22.8; Lun. 2.18-20Ankadalira Mulungu; ampulumutsetu tsopano Mulunguyo, ngati amamkondadi; paja ankati, Ndine Mwana wa Mulungu!” 44Zigaŵenga zimene adaazipachika pamodzi ndi Yesu zija, nazonso zinkamunyoza chimodzimodzi.
Kufa kwa Yesu
(Mk. 15.33-41; Lk. 23.44-49; Yoh. 19.28-30)
45Kuyambira pa 12 koloko masana mpaka pa 3 koloko, padaagwa mdima pa dziko lonse. 46#Mas. 22.1Tsono nthaŵi ili ngati 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eli, Eli, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?” 47Atamva mauwo, ena amene adaaimirira pamenepo adati, “Munthuyu akuitana Eliya.” 48#Mas. 69.21Motero wina adathamanga nakatenga chinkhupule. Adachiviika m'vinyo wosasa, nkuchitsomeka ku bango nampatsira, kuti amwe. 49Koma ena adati, “Taima, tiwone ngati Eliya abweredi kudzampulumutsa.” 50Koma Yesu adafuulanso kwakukulu, napereka mzimu wake.
51 #
Eks. 26.31-33
Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika. 52Manda adatsekuka ndipo anthu a Mulungu ambiri amene anali atamwalira kale, adauka kwa akufa. 53Adatuluka m'manda, ndipo Yesu atauka kwa akufa, iwo adaloŵa mu Yerusalemu, Mzinda Wopatulika, anthu ambiri nkumaŵaona.
54Mkulu wa asilikali ndiponso amene anali naye polonda Yesu, ataona chivomezi chija ndi zina zonse zimene zidaachitika, adachita mantha kwambiri nati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.” 55#Lk. 8.2, 3Patali poteropo padaali azimai ambiri akungoyang'anitsitsa. Iwoŵa ndi amene adaatsatira Yesu kuchokera ku Galileya ndi kumamtumikira. 56Pakati pao panali Maria wa ku Magadala, Maria mai wa Yakobe ndi Yosefe, ndiponso mai wa ana a Zebedeo.#27.56: Ana a Zebedeo: Onani mau ofotokozera Mt. 20.20.
Yesu aikidwa m'manda
(Mk. 15.42-47; Lk. 23.50-56; Yoh. 19.38-42)
57Chisisira chitagwa, kudafika munthu wina wolemera, wochokera ku Arimatea, dzina lake Yosefe. Nayenso anali wophunzira wa Yesu. 58Iyeyu adakapempha mtembo wa Yesu kwa Pilato. Pilato adalamula kuti ampatse mtembowo. 59Tsono Yosefe adautenga, naukulunga m'nsalu yoyera yabafuta. 60Adakauika m'manda ake atsopano ochita chosema m'thanthwe. Tsono adagubuduzira chimwala pa khomo kuti atseke pamandapo, nachoka. 61Maria wa ku Magadala ndi Maria wina uja anali pomwepo atakhala pansi kuyang'anana ndi mandawo.
Aika alonda pa manda a Yesu
62M'maŵa mwake, litapita tsiku lokonzekera Sabata, akulu a ansembe pamodzi ndi Afarisi adasonkhana napita kwa Pilato. 63#Mt. 16.21; 17.23; 20.19; Mk. 8.31; 9.31; 10.33, 34; Lk. 9.22; 18.31-33Adamuuza kuti, “Bwana, tikukumbukira kuti munthu wonyenga uja akali moyo ankati, ‘Patapita masiku atatu, ndidzaukanso.’ 64Tsono mulamule kuti azilondapo pamanda pake mpaka mkucha. Tikuwopa kuti ophunzira ake angadzabwere nkudzaba mtembo wake, kenaka namadzauza anthu kuti ‘Iye uja wauka kwa akufa.’ Apo kunyenga kotsirizaku kudzakhala koipa zedi kupambana koyamba kuja.” 65Pilato adaŵauza kuti, “Paja alonda muli nawo. Pitani, kalondeni pamandapo monga mukudziŵira.” 66Iwo adapitadi, nakatseka manda kolimba posindikiza chizindikiro pa chimwala chotsekeracho. Kenaka adasiya asilikali akulonda pomwepo.
Currently Selected:
Mt. 27: BLY-DC
Highlight
Copy
Compare
Share
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: