YouVersion Logo
Search Icon

Mt. 2

2
Alendo ochokera kuvuma
1Yesu adabadwira m'mudzi wa Betelehemu, m'dziko la Yudeya, pa nthaŵi imene Herode anali mfumu ya dzikolo. Ndiye kudaabwera akatswiri ena a nyenyezi ku Yerusalemu kuchokera kuvuma. 2Iwowo ankafunsa kuti, “Ali kuti mwana amene adabadwa kuti adzakhale Mfumu ya Ayuda? Ife tidaona nyenyezi yake ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza.” 3Mfumu Herode atamva zimenezi, adavutika kwambiri ndipo anthu ena onse a m'Yerusalemu nawonso adavutika nazo. 4Tsono Herodeyo adasonkhanitsa akulu onse a ansembe ndi aphunzitsi onse a Malamulo a Mose, naŵafunsa kuti, “Kodi paja adati Mpulumutsi wolonjezedwa ndi Mulungu uja adzabadwira kuti?” 5Iwo adati, “M'mudzi wa Betelehemu ku Yudeya. Pajatu mneneri adalemba kuti,
6 # Mik. 5.2 “ ‘Iwe Betelehemu wa m'dziko la Yuda,
sindiwe wamng'ono konse pakati pa akulu olamulira Yuda.
Pakuti kwa iwe kudzachokera mtsogoleri
pamene adzalamulira anthu anga Aisraele.’ ”
7Pamenepo Herode adaŵaitanira paseri akatswiri a nyenyezi aja, naŵafunsitsa za nthaŵi yeniyeni imene adaaiwonera nyenyeziyo. 8Kenaka adaŵatumiza ku Betelehemu nkuŵauza kuti, “Pitani, kafunsitseni za mwanayo. Mukakampeza, mudzandidziŵitse, kuti inenso ndidzapite kukampembedza.” 9Anthu aja atamva mau a mfumu, adanyamuka. Nyenyezi imene adaaiwona kuvuma ija idaŵatsogolera mpaka idakafika nkukaima pamwamba pa malo amene panali mwanayo. 10Ataiwona nyenyeziyo, adasangalala kwabasi. 11Adaloŵa m'nyumba, naona mwanayo ali ndi Maria mai wake, ndipo adagwada nampembedza. Kenaka adamasula chuma chao, nampatsa mitulo ya golide, lubani ndi mafuta onunkhira a mure.
12Mulungu adaŵachenjeza m'maloto kuti asadzerekonso kwa Herode kuja. Motero adadzera njira ina pobwerera kwao.
Makolo a Yesu athaŵira naye ku Ejipito
13Atapita akatswiri a nyenyezi aja, mngelo wa Ambuye adaonekera Yosefe m'maloto. Adamuuza kuti, “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mai wake, uthaŵire ku Ejipito. Ukakhale kumeneko mpaka ndidzakuuze, popeza kuti Herode azidzafunafuna mwanayu kuti amuphe.” 14Apo Yosefe adadzuka usiku womwewo, nkutenga mwanayo ndi mai wake kupita ku Ejipito. 15#Hos. 11.1Adakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira, kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Ndidaitana Mwana wanga kuti atuluke ku Ejipito.”
Herode apha ana
16Herode atazindikira kuti akatswiri a nyenyezi aja adampusitsa, adatuma anthu ku Betelehemu ndi ku midzi yonse yozungulira, kuti akaphe ana aamuna onse a zaka ziŵiri kapena kucheperapo. Zaka zimenezi adaaŵerengera potsata m'mene adaamvera kwa akatswiri aja za nthaŵi imene iwowo adaaiwonera nyenyeziyo. 17Pamenepo zidachitikadi zimene mneneri Yeremiya adaanena kuti,
18 # Yer. 31.15 “Mau akumveka ku Rama,
kulira ndi kubuma kwambiri:
Rakele akulira ana ake.
Akukana kumtonthoza,
chifukwa ana ake asoŵa.”
Makolo a Yesu abwerera naye kuchokera ku Ejipito
19Herode atamwalira, mngelo wa Ambuye adaonekera Yosefe m'maloto ku Ejipito. 20Adamuuza kuti, “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mai wake, ubwerere ku Israele. Aja ankafuna kumupha mwanayu adafa.” 21Apo Yosefe adanyamuka, nkutenga mwana uja ndi mai wake, kubwerera ku Israele. 22Koma atamva kuti Arkelao ndiye mfumu ya ku Yudeya m'malo mwa bambo wake Herode, adaopa kupita kumeneko. Tsono atalandira chenjezo kwa Mulungu m'maloto, adapita ku dera la Galileya. 23#Mk. 1.24; Lk. 2.39; Yoh. 1.45Kumeneko adakakhala ku mudzi wina dzina lake Nazarete, kuti zipherezere zimene aneneri adaanena kuti, “Adzatchedwa Mnazarete.”#2.23 Mnazarete: Gwero la dzina loti Nazarete pa chiyuda ndi chiphukira, ndipo mau ameneŵa akulozera pa Yes. 11.1. (Onaninso Yes. 53.2; Lk. 2.4)

Currently Selected:

Mt. 2: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy