YouVersion Logo
Search Icon

AROMA 16

16
Zolawirana
1Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wamkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkrea; 2#Afi. 2.29kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zilizonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe. 3#Mac. 18.2Mupereke moni kwa Prisika ndi Akwila, antchito anzanga mwa Khristu Yesu, 4amene anapereka khosi lao chifukwa cha moyo wanga; amene ndiwayamika, si ine ndekha, komanso Mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu; 5#1Ako. 16.19ndipo mupereke moni kwa Mpingo wa Ambuye wa m'nyumba mwao. Moni kwa Epeneto wokondedwa wanga, ndiye chipatso choundukula cha Asiya cha kwa Khristu. 6Moni kwa Maria amene anadzilemetsa ndi ntchito zambiri zothandiza inu. 7Moni kwa Androniko ndi Yunia, anansi anga, ndi andende anzanga, amene ali omveka mwa atumwi, amenenso ananditsogolera ine mwa Khristu. 8Moni kwa Ampiliato wokondedwa wanga mwa Ambuye. 9Moni kwa Urbano wantchito mnzathu mwa Khristu, ndi Stakisi wokondedwa wanga. 10Moni kwa Apelesi, wovomerezedwayo mwa Khristu. Moni iwo a kwa Aristobulo. 11Moni kwa Herodiono, mbale wanga. Moni iwo a kwa Narkiso, amene ali mwa Ambuye. 12Moni kwa Trifena, ndi Trifosa amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye. Moni kwa Perisi, wokondedwayo amene anagwiritsa ntchito zambiri mwa Ambuye. 13Moni kwa Rufu, wosankhidwayo mwa Ambuye, ndi amai wake ndi wanga. 14Moni kwa Asinkrito, Filegoni, Heremesi, Patrobasi, Herimasi ndi abale amene ali nao. 15Moni Filologo ndi Juliya, Nereo ndi mlongo wake, ndi Olimpasi, ndi oyera mtima onse ali pamodzi nao. 16#1Ako. 16.20Mupatsane moni wina ndi mnzake ndi kupsompsona kupatulika. Mipingo yonse ya Khristu ikupatsani moni.
17 # Mac. 15.1, 5, 24 Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo. 18#Afi. 3.19; Akol. 2.4Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa. 19#Mat. 10.16; Aro. 1.8Pakuti kumvera kwanu kunabuka kwa anthu onse. Chifukwa chake ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pa zabwino, koma ozungulidwa pa zoipa. 20#Aro. 15.33; 1Ako. 16.23Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino.
Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. 21#Mac. 16.1; 17.5Timoteo wantchito mnzanga akupatsani moni; ndi Lusio ndi Yasoni ndi Sosipatere, abale anga. 22Ine Tersio, ndilikulemba kalata ameneyu, ndikupereka moni mwa Ambuye. 23#Mac. 19.22; 1Ako. 1.14Gayo, mwini nyumba wolandira ine, ndi Mpingo wonse wa Ambuye, akupereka moni. Erasto, ndiye woyang'anira mudzi, akupereka moni, ndiponso Kwarto mbaleyo.#16.23 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 24 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Amen.
25 # Aro. 2.16; Aef. 3.3-6, 9, 20 Ndipo kwa Iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa Uthenga wanga Wabwino, ndi kulalikira kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso la chinsinsi chimene chinabisika mwa nthawi zonse zosayamba, 26#Aef. 1.9koma chaonetsedwa tsopano, ndi kudziwidwa kwa anthu a mitundu yonse mwa malembo a aneneriwo, monga mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti amvere chikhulupiriro; 27#1Tim. 1.17kwa Mulungu wanzeru yekhayo, mwa Yesu Khristu, kwa yemweyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.

Currently Selected:

AROMA 16: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in