YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 26

26
Akulu a Ayuda apangana amgwire Yesu
(Mrk. 14.1-2; Luk. 22.1-2; Yoh. 11.47)
1Ndipo panali pamene Yesu anatha mau onse amenewa, anati kwa ophunzira ake, 2Mudziwa kuti akapita masiku awiri, Paska afika, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kupachikidwa pamtanda. 3#Mac. 4.25-27Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa; 4nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi chinyengo, namuphe. 5Koma ananena iwo, pa nthawi la chikondwerero iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.
Yesu m'nyumba ya Simoni wakhate
(Mrk. 14.3-9; Yoh. 12.1-8)
6 # Yoh. 12.4-8 Ndipo pamene Yesu anali m'Betaniya, m'nyumba ya Simoni wakhate, 7anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa ya alabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatali, nawatsanulira pamutu pake, m'mene Iye analikukhala pachakudya. 8Koma m'mene ophunzira anaona, anada mtima, nanena, Chifukwa ninji kuononga kumeneku? 9Pakuti mafuta awa akadagulitsa ndalama zambiri, ndi kuzipatsa anthu aumphawi. 10Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumvutiranji mkaziyu? Popeza andichitira Ine ntchito yabwino. 11Pakuti nthawi zonse muli nao aumphawi pamodzi nanu; koma simuli ndi Ine nthawi zonse. 12Pakuti mkaziyo, m'mene anathira mafuta awa pathupi panga, wandichitiratu ichi pa kuikidwa kwanga. 13Indetu ndinena kwa inu, kumene kulikonse Uthenga uwu Wabwino udzalalikidwa m'dziko lonse lapansi, ichi chimene mkaziyo anachitachi chidzakambidwanso chikumbukiro chake.
Mphotho ya kumpereka Yesu
(Mrk. 14.10-11; Luk. 22.3-6)
14Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudasi Iskariote, anamuka kwa ansembe aakulu, 15nati, Mufuna kundipatsa chiyani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu. 16Ndipo kuyambira pamenepo iye anafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye.
Paska wotsiriza
(Mrk. 14.12-21; Luk. 22.7-14, 21-23; Yoh. 3.21-30)
17 # Eks. 12.18 Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda chotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paska, kuti mukadye? 18Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wangana, mukati kwa Iye, Mphunzitsi anena, Nthawi yanga yayandikira; ndidzadya Paska kwanu pamodzi ndi ophunzira anga. 19Ndipo ophunzira anachita monga Yesu anawauza, nakonza Paska.
20 # Mrk. 14.17-21 Ndipo pakufika madzulo, Iye analinkukhala pachakudya pamodzi ndi ophunzira khumi ndi awiri; 21ndipo m'mene analinkudya, Iye anati, Indetu ndinena kwa inu, mmodzi wa inu adzandipereka Ine. 22Ndipo iwo anagwidwa ndi chisoni chachikulu, nayamba kunena kwa Iye mmodzimmodzi, Kodi ndine, Ambuye? 23#Mas. 41.9; Yoh. 13.18Ndipo Iye anayankha nati, Iye amene asunsa pamodzi ndi Ine dzanja lake m'mbale, yemweyu adzandipereka Ine. 24Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa. 25Ndipo Yudasi, womperekayo anayankha nati, Kodi ndine, Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero.
Mgonero wa Ambuye
(Mrk. 14.22-26; Luk. 22.15-20; 1Ako. 11.23-25)
26 # Mrk. 14.22 Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa. 27#Mrk. 14.23Ndipo pamene anatenga chikho, anayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ichi inu nonse, 28#Eks. 24.8; Yer. 31.31; Aro. 5.15pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo. 29#Mrk. 14.25Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso chipatso ichi champesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa chatsopano, pamodzi ndi inu, mu Ufumu wa Atate wanga.
30 # Mrk. 14.26 Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kunka kuphiri la Azitona.
Yesu achenjeza Petro
(Mrk. 14.27-31; Luk. 22.31-34; Yoh. 13.36-38)
31 # Zek. 13.7; Mrk. 14.27 Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa,
Ndidzakantha mbusa,
ndipo zidzabalalika
nkhosa za gulu.
32 # Mat. 28.7; Mrk. 14.28 Koma nditauka ndidzatsogolera inu ku Galileya. 33Koma Petro ananena kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse. 34Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu. 35Petro ananena kwa Iye, Ngakhale ine ndikafa ndi Inu, sindidzakukanani Inu iai. Anateronso ophunzira onse.
Yesu m'Getsemani
(Mrk. 14.32-42; Luk. 22.39-46; Yoh. 18.1)
36 # Mrk. 14.32-35 Pomwepo Yesu anadza ndi iwo kumalo otchedwa Getsemani, nanena kwa ophunzira ake, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere. 37#Mat. 4.21Ndipo anatenga Petro ndi ana awiri a Zebedeo pamodzi naye, nayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuthedwa nzeru. 38#Yoh. 12.27Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa; khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine. 39#Mrk. 14.36; Aheb. 5.7Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu. 40Ndipo anadza kwa ophunzira, nawapeza iwo ali m'tulo, nanena kwa Petro, Nkutero kodi? Simukhoza kuchezera ndi Ine mphindi imodzi? 41#Mrk. 13.33; Mrk. 14.38; Aef. 6.18Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka. 42Anamukanso kachiwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ichi sichingandipitirire, koma ndimwere ichi, kufuna kwanu kuchitidwe. 43Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali m'tulo, pakuti zikope zao zinalemera ndi tulo. 44Ndipo anawasiyanso, napemphera kachitatu, nateronso mau omwewo. 45Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a ochimwa. 46Ukani, timuke; taonani, iye wakundipereka wayandikira.
Amgwira Yesu
(Mrk. 14.43-50; Luk. 22.47-53; Yoh. 18.2-11)
47Ndipo Iye ali chilankhulire, onani, Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kuchokera kwa ansembe aakulu ndi akulu a anthu. 48#2Sam. 20.9Koma wompereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona ndiyeyo, mumgwire Iye. 49Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuoneni, Rabi; nampsompsonetsa. 50Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye. 51Ndipo onani, mmodzi wa iwo anali pamodzi ndi Yesu, anatansa dzanja lake, nasolola lupanga lake, nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake. 52#Gen. 9.6Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza lupanga lako m'chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi lupanga. 53#2Maf. 6.17Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri? 54#Yes. 53.7-10Koma pakutero malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho? 55Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala m'Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwira. 56#Yes. 53.7-10Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.
Yesu kubwalo la akulu a Ayuda
(Mrk. 14.53-56; Luk. 22.63-71; Yoh. 18.12-27)
57Ndipo iwo akugwira Yesu ananka naye kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akulu omwe. 58Koma Petro anamtsata kutali, kufikira kubwalo la mkulu wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone chimaliziro. 59Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye; 60#Mas. 27.12; Mrk. 14.55koma sanaupeze zingakhale mboni zonama zambiri zinadza. Koma pambuyo pake anadza awiri, 61#Mat. 27.40; Yoh. 2.19nati, Uyu ananena kuti, Ndikhoza kupasula Kachisi wa Mulunguyu, ndi kummanganso masiku atatu. 62Ndipo mkulu wa ansembe anaimirira, nati kwa Iye, Suvomera kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa akunenera Iwe? 63#Yes. 53.7; Mat. 27.12, 14Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu. 64#Dan. 7.13; Luk. 21.27Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu ali kukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba. 65#2Maf. 19.1Pomwepo mkulu wa ansembe anang'amba zovala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo; 66#Lev. 24.16muganiza bwanji? Iwo anayankha nati, Ali woyenera kumupha. 67#Yes. 50.6Pomwepo iwo anathira malovu pankhope pake, nambwanyula Iye; ndipo ena anampanda khofu, 68#Mrk. 14.65nati, Utilote ife, Khristu Iwe; wakumenya Iwe ndani?
Petro akana Yesu
(Mrk. 14.66-72; Luk. 22.54-62; Yoh. 18.15-18, 25-27)
69 # Mrk. 14.66 Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya. 70Koma iye anakana pamaso pa anthu onse, kuti, Chimene unena sindichidziwa. 71Ndipo pamene iye anatuluka kunka kuchipata, mkazi wina anamuona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo. 72Ndipo anakananso ndi chilumbiro, kuti, Sindidziwa munthuyo. 73Ndipo popita nthawi yaing'ono, iwo akuimapo anadza, nati kwa Petro, Zoonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe. 74#Mrk. 14.71Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira. 75#Mrk. 14.30; Luk. 22.61-62; Yoh. 13.38Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anatulukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima.

Currently Selected:

MATEYU 26: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy