MATEYU 24:9-11
MATEYU 24:9-11 BLPB2014
Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa. Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake. Ndipo aneneri onama ambiri adzauka, nadzasokeretsa anthu ambiri.