YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 14

14
Herode amupha Yohane Mbatizi
(Mat. 6.14-29; Luk. 3.19-20; 9.7-9)
1 # Mrk. 6.14 Nthawi imeneyo Herode mfumu anamva mbiri ya Yesu, 2nanena kwa anyamata ake, Uyo ndiye Yohane Mbatizi; anauka kwa akufa; ndipo chifukwa cha ichi zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye. 3#Mrk. 6.17Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake Filipo. 4#Lev. 20.21Pakuti Yohane ananena kwa iye, Sikuloledwa kwa iwe kukhala naye. 5#Luk. 20.6Ndipo pofuna kumupha iye, anaopa khamu la anthu, popeza anamuyesa iye mneneri.
6Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi anavina pakati pao, namkondweretsa Herode. 7Pomwepo iye anamlonjeza chilumbirire, kumpatsa iye chimene chilichonse akapempha. 8Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi. 9Ndipo mfumuyo anagwidwa ndi chisoni; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo anali naye pachakudya, analamulira upatsidwe; 10ndipo anatumiza mnyamata, namdula mutu Yohane m'nyumba yandende. 11Ndipo anautenga mutu wake m'mbalemo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amake. 12Ndipo ophunzira ake anadza, natola mtembo, nauika; ndipo anadza nauza Yesu.
Yesu achulukitsa mikate poyamba paja
(Mrk. 6.30-44; Luk. 9.10-17; Yoh. 6.1-14)
13 # Mrk. 6.32 Ndipo Yesu pakumva, anachokera kumeneko m'ngalawa, kunka kumalo achipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kuchokera m'midzi. 14#Mat. 9.36Ndipo Iye anatuluka, naona khamu lalikulu la anthu, nachitira iwo chifundo, nachiritsa akudwala ao. 15#Mrk. 6.35Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ake anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga chipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite kumidzi kukadzigulira okha kamba. 16Koma Yesu anati kwa iwo, Iwo alibe chifukwa cha kumukira, apatseni ndinu adye. 17Koma iwo ananena kwa Iye, Ife tilibe kanthu pano koma mikate isanu, ndi nsomba ziwiri. 18Ndipo Iye anati, Mudze nazo kuno kwa Ine. 19#Mat. 15.36Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo. 20Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, nadzala madengu khumi ndi iwiri. 21Ndipo anadyawo anali amuna monga zikwi zisanu, kuwaleka akazi ndi ana.
Yesu ayenda panyanja
(Mrk. 6.45-46; Yoh. 6.15-21)
22Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera Iye kutsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke. 23#Mrk. 6.46Ndipo pamene Iye anawauza makamuwo, anakwera m'phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha. 24Koma pomwepo ngalawa idafika pakati pa nyanja, yozunzika ndi mafunde; pakuti mphepo inadza mokomana nao. 25Ndipo pa ulonda wachinai wa usiku, Iye anadza kwa iwo, nayenda pamwamba pa nyanja. 26#Yob. 9.8Koma m'mene ophunzirawo anamuona Iye, alikuyenda pamadzi, ananthunthumira, nati, Ndi mzukwa! Ndipo anafuula ndi mantha. 27Koma pomwepo Yesu analankhula nao, nati, Limbani mtima; ndine; musaope. 28Ndipo Petro anamyankha Iye nati, Ambuye, ngati ndinutu, mundiuze ndidze kwa Inu pamadzi. 29Ndipo Iye anati, Idza. Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu. 30Koma m'mene iye anaiona mphepo, anaopa; ndipo poyamba kumira, anafuula, nati, Ambuye, ndipulumutseni ine! 31Ndipo pomwepo Yesu anatansa dzanja lake, namgwira iye, nanena naye, Iwe wokhulupirira pang'ono, wakayikiranji mtima? 32Ndipo pamene iwo analowa m'ngalawamo, mphepo inaleka. 33#Mas. 2.7; Mat. 16.16; 26.63; Mrk. 1.1; Luk. 4.41; Yoh. 11.27; Aro. 1.4Ndipo iwo amene anali m'ngalawamo anamgwadira, nanena, Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.
34Ndipo pamene iwo anaoloka, anafika kumtunda, ku Genesarete. 35Ndipo m'mene amuna a pamenepo anamzindikira, anatumiza konse kudziko lonse lozungulira, nadza nao kwa Iye onse akukhala ndi nthenda; 36#Mat. 9.20; Mrk. 3.10; Luk. 6.19; Mac. 19.12ndipo anampempha Iye, kuti akhudze yokha mphonje ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.

Currently Selected:

MATEYU 14: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy